Yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha Democratic Progressive-DPP a Kondwani Nankhumwa ati adzapikisana nawo pa chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino chomwe chikuyembekezeka kuchitika chaka cha mawa.
A Nankhumwa, omwe anachotsedwa m’chipani cha DPP kaamba kogawukira komanso kudelera utsogoleri wake, anena izi lero ku Ndirande- Malabada muzinda wa Blantyre.
Malingana ndi a Nankhumwa, akuluakulu a chipani cha DPP anawachotsa m’chipanichi kamba koti anaonetsa chidwi chofuna kudzapikisana nawo pa chisankho cha mtsogoleri wa chipani cha DPP.
A Nankhumwa, omwe akuyembekezereka kuwuza a Malawi za tsogolo lawo pa ndale sabata ino, ati maloto omwe anali nawo odzapikisana nawo pa chisankho cha mtsogoleri sanafe.
Nankhumwa, omwenso ndi phungu wa m’dera la pakati m’boma la Mulanje, anachotsedwa chipanichi pamodzi ndi anthu ena, omwe ndi kuphatikizapo Grezelder Jeffrey, Cecilia Chazama, Nicholas Dausi mwa ena.
The post Ndizapikisana nawo pa pa chisankho cha mtsogoleri wa dziko-Nankhumwa appeared first on Malawi Voice.