Zaka ziwiri kwa akuba pa foni

Zaka ziwiri kwa akuba pa foni

Bwalo la Nsanje Third Grade Magistrate lalamula amuna awiri kukagwira ukaidi kwa miyezi 24 atawapeza wolakwa pa mlandu woba mafoni.

Yemwe amaimira boma pa mlanduwu a Innocent Banda anauza bwalolo kuti awiriwa, White Potifala ndi Nkhonde Wisted, pa 12 July 2023 anafika pa msika wa Tengani m’bomalo ngati ofuna kutchajitsa mafoni komanso kuti ametedwe m’malo wometera a Shadreck Mussa.

Sergeant Banda anati kenako Potifala anatuma Mussa kuti akamugulire chakumwa cha mtundu wa Frozzy ndipo iwo anakwanitsa kuba malamya wokwanira 7 a K734, 500 ndipo anathawira ku Blantyre.

Iwo anati Potifala anagwidwa pa msika wa Thabwa ku Chikwawa ndi lamya mmodzi wamtundu wa Samsung Galaxy A13 yandalama zokwanira K250, 000 ya a Kennedy Petro Yohane.

PA bwalo la milandu awiriwa anaukana mlandu wakuba mosemphana ndi gawo 278 ya malamulo aakulu a dziko lino ndipo woimira boma anabweretsa mboni zake zitatu zomwe zinapherezera kuti mlanduwu unapalamulidwadi.

Zinadziwika m’bwalolo kuti malamya ena 6 anagulitsidwa ku Blantyre.

Popereka madandaulo awo atawapeza olakwa, Potifala ndi Wisted anapempha chifundo ponena kuti n’kuyamba kupalamula milandu komanso amayang’anira mabanja awo omwe avutike akatumizidwa ku ndende.

Koma Sergeant Banda anatsutsa izi ponena kuti amunawa kupalamula mlandu ngati uwu ndi kachitatu. Iye anapempha chilango chokhwima chomwe chingachititse anthu ena kuopa kupalamula milandu ya mtunduwu.

Sergeant Banda anati zikuonetsa kuti amuna awiriwa anachita kukonzekera bwino lomwe kupalamula mulanduwu popeza anachita kuchoka ku Blantyre ndi kufika ku Nsanje kukapalamula mlanduwu.

Woweruza Haneef Ngundende anagwirizana ndi woimira boma ponena kuti anthu ngati awa ndi oipa kwambiri popeza amachititsa kuti anthu omwe ali ndi malo wotchajira lamya akhale ndi milandu ya ndalama zochuluka pofuna kubweza malamya omwe amakhala akubedwa.

Mwaichi Ngundende analamula Potifala ndi Wisted kuti akagwire ukaidi kwa zaka ziwiri kuti andipsi ena atengerepo phunziro.

Potifala wa zaka 23 amachokera kwa Nyenyezi T/A Mlolo pomwe Wisted wa zaka 25 kwawo ndikwa Sorgin T/A Mbenje m’boma la Nsanje.

The post Zaka ziwiri kwa akuba pa foni appeared first on The Nation Online.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください