‘Tonse ikubisa thumba la tambe’

 ‘Tonse ikubisa thumba la tambe’

 Abwenzi akuluakulu mumgwi r izano wa Tonse Alliance a UTM komanso People’s Party (PP) akana kulankhulapo p a z omwe ada l ankhul a mtsogoleri wadziko lino a Lazarus Chakwera kuti aimanso mu 2025 ndipo adzalamulira mpaka mu 2030.

A Chakwera adalankhula izi pa 14 May 2024 kumwambo wokumbukira mtsogoleri woyamba wa dziko lino Dr Hastings Kamuzu Banda ku Kamuzu Stadium mumzinda wa Blantyre.

A Chilima ndi a Chakwera tsiku lokhazikitsa Tonse Alliance

“Kuchokera mmwezi wa October 2025, ine ndidzakhala ndikupitiriza zitukuko zomwe ndidayamba kale. Kaya amene akudza ndi ndale za miseche afune kaya asafune, ndipitiriza zitukuko zimene zilipo mpaka 2030,” adatero iwo.

Izi zikusemphana ndi zomwe adanena wachiwiri wawo a Saulos Chilima yemwe ndi mtsogoleri wa UTM kuti mgwirizano wawo udali woti m’chaka cha 2025, a Chilima ndiwo adzaimire Tonse Alliance.

Koma mlembi wamkulu wachipani cha UTM mayi Patricia Kaliati omwe adali kumwambowo ati iwo sadamve zomwe adanena a Chakwera k o t e r o n ’ k o v u t a kuthirirapo ndemanga pa nkhaniyo.

“ S i n d i d a m v e k o z i m e n e z o n d i y e sindiyankha pa zinthu zomwe sindidamve, m w i n a m u t a f u n s a anzanthu mumgwirizano wa To n s e A l l i a n c e ngati adamvako ndipo kuti zikutanthauzanji zimenezo,” adatero a Kaliati.

Mneneri wa chipani cha PP a Ackson Kalaile Banda adati mpovuta kuyankhapo chifukwa chomwe iwo akudziwa n’choti ali mumgwirizano basi.

“Tili mu mgwirizano ndipo chipani chilichonse chikhoza kunena zomwe chikufuna ngati chipani. Apapa a Chakwera a d a l a n k h u l a n g a t i mtsogoleri wa dziko komanso wa chipani cha MCP osati Tonse Alliance ndiye sitingayankhepo,” adatero a Kalaile Banda.

Koma kadaulo pa ndale a Nandine Patel adati n’zoona kuti a Chakwera ali ndi ufulu woimanso kachiwiri koma amayenera kudikira kovenshoni ya chipani chawo kuti akaone ngati nthumwi zikawapatsenso mphamvu zoziimiriranso.

“Ine ndikuona kuti a l a n k h u l a m s a n g a chifukwa sadapange komvenshoni, n’kutheka kuti alipo ena omwe akufuna kudzapikisana nawo ku kovenshoniko ndiye akadadekha kaye asadayambe kulankhula choncho,” adatero a Patel.

K o m a p a m s o n k h a n o w o , i w o a d a u z i l i r a n s o pokumbutsa zipani zomwe zili mu Tonse Alliance kuti ulendo w a w o a ku p i t i r i r a kuyendera limodzi dipo asalole kuti anthu ena awasokoneze maganizo pa zaubale wawo.

“ To n s e o m w e tidayambira limodzi ku m a n g a n s o d z i ko lino tisalole kuti ena atigawanitse. Tilibe nthawi yolimbirana mipando koma kuwonetsetsa kuti Amalawi ali ndi chakudya ndi chitukuko,” adatero a Chakwera.

A Chilima omwenso a d a l i n a w o p a mwambowo amaoneka osatekeseka ndi zomwe zinkanenedwazo.

Chaka chathachi mlembi wamkulu wa MCP a Eisenhower Mkaka adati sakudziwapo kal ikonse kokhudza mgwirizano woti a Chilima adzaimirira Ton s e A l l i a n c e mu 2025.

The post  ‘Tonse ikubisa thumba la tambe’ first appeared on Nation Online.

The post  ‘Tonse ikubisa thumba la tambe’ appeared first on Nation Online.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください