Akadaulo a zandale ati mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera akuchedwa kuthothola mphamvu zina monga momwe adalonjezera.
Bungwe la akadaulowo pa ndale la Political Science Association (PSA) lati papita nthawi kuchokera pomwe apulezidenti adalonjeza kuti adzathothola mphamvu zina koma kuli ziii mpaka lero.
Mlembi wamkulu wa bungwelo a Makhumbo Munthali ati m’malamulo a dziko lino zilimo zoti mtsogoleri akhoza kuthothola mphamvu kuti zina m’dziko ziyende bwino.
A Chakwera kuonekera ku Nyumba ya Malamulo
Mmbuyomo mneneri wa apulezidenti a Anthony Kasunda adayankha funsoli ponena kuti apulezidenti akukwaniritsa lonjezo lawo chifukwa mwa zina amakaonekera ku Nyumba ya Malamulo monga malamulo amanenera.
Koma a Munthali ati: “Si zomveka kunena kuti poti apulezidenti amakaonekera kunyumbayo kapena ku bungwe lolimbana ndi katangale la ACB ndiye kuti athothola mphamvu ayi. Izizi zilimo kale m’malamulo kuti amayenera kutero.”
A Munthali adati n’kofunikanso kumvetsetsa mtundu wa mphamvu zomwe apulezidenti akuyenera kuthothola chifukwa pali mphamvu za ofesi komanso pali mphamvu zongovala.
“Mphamvu zomwe anthu akufuna apulezidenti atathotholako ndi za ofesi chifukwa n’zomwe zimagwira ntchito ngati lamulo,” adatero a Munthali.
Lolemba lapitali a Kasunda adati apulezidenti adathothola mphamvu zina chifukwa salowerera ntchito za ACB, apolisi komanso ofesi yomva madandaulo a anthu ya Ombudsman.
Iwo adati n’zosafuna kuuzidwa kuti apulezidenti amakaonekera n’kukayankha mafunso ku Nyumba ya Malamulo monga momwe malamulo amanenera.
Ndime 89 (4) ya malamulo a dziko lino amati Pulezidenti akuyenera kupita ku Nyumba ya Malamulo kukayankha mafunso ngati nyumbayo yoona kuti n’kufunika kutero pogwiritsa ntchito malamulo ake.
Pa 6 September 2020 a Chakwera polankhula ku mtundu wa Amalawi adati mtsogoleri akakhala ndi mphamvu zambiri zinthu zina zimaonongeka m’dziko.
Kadaulo winanso pandale a Humphrey Mvula wati uthenga wa a Chakwera wa pa 6 September 2020 udali wongofuna kumvetsa kunzuna Amalawi omwe adawavotera pachisankho.
Pomasulira mawu awo, a Mvula adati sichamasewera kuthothola mphamvu za utsogoleri chifukwa n’zofunika kuzukuta malamulo mofatsa zomwe zimatenga nthawi kuti zitheke.
The post ‘Sosolani mphamvu bwana’ appeared first on The Nation Online.