Mfumu yaikulu Chimombo yam’boma la Nsanje yadzudzula nthambi ya apolisi kuti yakondera padongosolo lopereka nyota zatsopano kwa apolisi m’dziko muno.
Mfumuyi yasonyeza kusakhutiraku kutsatira malipoti oti apolisi awiri okha m’boma la Nsanje ndiwo akwezedwa pantchito mwa apolisi opyola 800 omwe alandira nyota zatsopano m’dziko muno.
Mfumuyi yati zomwe zachitikazi ziri ndikuthekera kobwezera mbuyo magwiridwe antchito a apolisi zomwe zingasokoneze ntchito zachitetezo m’bomali.
Malingana ndi mfumu Chimombo nthambi ya apolisi ikuyenera kupereka mwayi ofanana kumaboma onse padongosolo lopereka nyota zatsopano kwa apolisi m’dziko muno.
Akuluakulu a nthambi yapolisi m’dziko muno sanayankhulepo kanthu pankhawa zomwe mfumuyi yapereka.-Capital FM
The post Nthambi ya Police ayithira mphepo kaamba kokondera appeared first on Malawi Voice.