Mtsogoleri wa aphungu achipani cha Democratic Progressive (DPP) ku nyumba ya malamulo, Mayi Mary Navicha wafunira zabwino a George Chaponda omwe asankhidwa kukhala mtsogoleri wa aphungu mnyumba ya malamulo.
Mayi Navicha, omwenso ndi phungu wa dera la nyumba ya malamulo la Thyolo Thava ayankhula lero ku Njamba mu mzinda wa Blantyre komwe chipanichi chachititsa msonkhano wa ndale.
Pa msonkhano’wu, mayi Navicha apepesaso kwa aMalawi ati kaamba koti iwo ndi aphungu amnzawo anasinthaa calender ya chisankho kufika mwezi wa September.
“Tinalakwitsa posintha kalendala ya chisankho. Timayenera kuvota sabata ya mmawa pa 20 May.”
Pamenepa, iwo anapempha aphungu onse omwe ali pa msonkhono-wu kuti ayime kusonyeza kupepesa pa zomwe zinachitikazi.
Iwo ati linali khumbo lawo kuti chaka chino cha 2024 akhale atatenga m’boma.
The post Navicha wafunira zabwino Chaponda appeared first on Malawi Voice.