Mwana apha bambo ake

 Mwana apha bambo ake

Apolisi m’boma la Lilongwe, akusaka mnyamata wa zaka 17 pomuganizira kuti anamenya ndi kupha bambo ake a zaka 33 chifukwa choti anamumana ndalama yomwe anawapempha.

Izi zinachitika kwa Chinsapo, mumzinda wa Lilongwe.

Wachiwiri kwa mneneri wa polisi m’boma la Lilongwe a Foster Benjamin atsimikiza kuti a Divala Chitsonga omwe anali woyendetsa minibasi anamenyedwa ndi chimtengo m’mutu Loweruka.

“Mnyamatayo anapempha ndalamazo kwa bambo ake kuti akasangalale ndi moyo. Koma bambowo anamukaniziratu zomwe sizinamusangalatse,” adatero a Benjamin.

Iwo adati apa mnyamatayo anawamenya bambowo ndi chimtengo pomwe amakakwera minibasi kuti azipita ku ntchito yawo.

“A Divala adakomoka pompo ndipo adamwalira akulandira thandizo pachipatala chachikulu cha Kamuzu mumzinda wa Lilongwe,” iwo adatero.

A Chitsonga amachokera m’mudzi mwa a Matewe, Mfumu Mlumbe, m’boma la Zomba.

Khalidwe la ana maka amuna kuvulaza ndi kupha makolo komanso abale awo latumphukira m’dziko muno.

Pomwe kwa Chimtsekwa Mfumu Chilooko, m’boma la Ntchisi, bambo wina wa zaka akuganiziridwa kuti anabaya ndi kupheratu mchimwene wake wa zaka 24 komanso kubaya ndi kuvulaza makolo ake a zaka 91, mwezi wa May chaka chino.

Apolisi m’boma la Ntchisi adatsimikiza kuti a Edward Chatambalala anachita izi ataledzera.

Pomwe mwezi wa April chaka chino, a Anthony Binoliyasi a zaka 35 omwe amachokera m’mudzi mwa Kumbeni, Mfumu Lulanga, m’boma la Mangochi akuganiziridwa kuti anapha bambo ake owabereka a zaka 67 chifukwa anawakaniza kukadula nzimbe ku dimba lawo.

Ndipo mwezi wa January, bambo wina wa zaka 22 anapha mchimwene wake wodwala matenda a mu ubongo wa zaka 27 ndi kumukwirira m’nyumba mwake pa zifukwa zosadziwika bwino.

Mwezi omwewo mnyamata winanso akuganiziridwa kuti anapha bambo awo powakankhira mumtsinje pomwe anasemphana nawo chichewa ku Lilongwe komweko.

Mchitidwewu ukupereka mantha mwa anthu akuluakulu omwe ati izi zikuchitika chifukwa cha chamba ndi mankhwala ozunguza bongo omwe achinyamata ena akugwiritsa ntchito masiku ano.

Malinga ndi a Mfumu Maliri a m’boma la Lilongwe komwe mchitidwewu wayalanso nthenje, makolo ambiri akudutsa m’nyengo zowawa ndi achinyamata awo.

Iwo adati vuto lagona poti achinyamatawa akaledzera ndi kusuta chamba akumazunguza makolo awo omwe.

A Maliri adati achinyamatawo kumaonera izi m’mafilimu komanso m’magulu a anzawo.

“Kale izi kunalibe, achinyamata ankalemekeza makolo awo ndipo ayi, ankawamvera osati zomwe zikuchitika masiku anozi,” anatero a Maliri. Iwo apempha boma kuti liwapatse achinyamata zochita kuti azikhala otanganidwa komanso azipeza ndalama zawo chifukwa mchitidwewu ukukulanso chifukwa cha ulova.

The post  Mwana apha bambo ake appeared first on The Nation Online.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください