Mpungwepungwe Pamaliro a Thomas Chibade

Kusamvana kwakula ku Area 50 mmudzi mwa Ngomani ku Lilongwe komwe kumakhala malemu Thomas Chibade pomwe khwimbi la anthu lakaniza akumbumba kunyamula maliro kuti akayikidwe Ku Zomba monga mwachikonzero.

Zinafika povuta poti mpaka akumbumba anawathawitsa ndikuwabisa pomwe okonda nyimbo za Thomas Chibade anafuna kuchitira ntopola achibale a Chibade kaamba koti achibarewa sanakonzeke zoyendetsa mwambowu paokha.

Ena ati anthu okonda nyimbo za chibade komanso bungwe la oyimba mdziko muno ndi amene anasonkhetsa ndalama zoyendetsera mwambowu.

M’modzi mwa akuluakulu akubungwe la MUM a Alex Mkalo ati pakadali pano akumbumba avomereza zoyika malirowo Ku Lilongwe ku Area 18 osati Ku Zomba komwe malemuwa amachokera.-MBC ONLINE

The post Mpungwepungwe Pamaliro a Thomas Chibade appeared first on Malawi Voice.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください