Mpungwepungwe ku msika wa fodya

 Mpungwepungwe ku msika wa fodya

Listen

Kudali mpungwepungwe kumsika wa fodya wa Kanengo mumzinda wa Lilongwe pomwe alimi adakwiya ndi mitengo ya fodya ndipo adauza ngakhale mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera kuti bola msikawo angoutseka.

Mpungwepungwe udabuka kaamba ka alimi makamaka omwe adali paokha osati pakontilakiti amene adati fodyayo amamugula mtengo wotsika kwambiri kuposa zolowa zochuluka zimene amalowetsa paulimiwu.

A Zakaliya kulankhula ndi a Chakwera
za mavuto a alimi

Kwa mphindi 15, mtsogoleri wa dziko linoyu adalephera kuzungulira mumzindawo pomwe alimi adali

Koma a Chakwera adadzudzula alimiwo kaamba koika zitsotso ndi zina zosakhudzana ndi fodya akamapita kumsika kuti ndizo zimachititsa mtengo utsike. Iye adati adati adadzionera yekha zinyalala zili thooo m’mabelo ena a fodya.

Koma mosabisa mawu, woimira alimiwo, a Musaiwale Zakaliya adati akudziwa kuti a Chakwera sadziwa za mavuto ena omwe alimi a fodya amakumana nawo ndipo adapempha kuti apatsidwe mpata wokakumana ndi a Chakwerawo kuti akawafotokozere zambiri.

“Zambiri sizimakupezani chifukwa oyenera kukuuzani amabisa, ndiye mutilole tidzabwere tokha kudzakufotokozerani mavuto athu kuti mutithandize,” adatero a Zakaliya.

Koma polankhula pamsonkhano umene adachititsa atatsegulira msikawo, a Chakwera adati n’zosatheka kukumana ndi alimiwo paokha.

“Alimi ambiri ali ndi mavuto kuno kwathu tsono sizingatheke kuti aliyense azibwera kudzakumana ndi mtsogoleri wa dziko. Chofunika n’kugwiritsa njira zokhazikika pofuna kuthana ndi madandaulo amene angakhalepo,” adatero iwo.

Ndipo a Zakaliya adati ngakhale makampani akwenza mtengo wogulira fodya pa kilogalamu, kusinthako sikudanunkhe kanthu chifukwa akwenza pang’ono moti alimiwo ankalingalira zoimitsa msikawo kuti akonze mitengo.

A Zakaliya adadzudzulanso boma kuti siliganizira kwambiri alimi a fodya chifukwa lidawakwezera mtengo wa fodya pang’ono poyerekeza ndi mbewu zina.

“Mbewu zina monga chimanga ndi soya mudakweza ndi ndalama zochuluka. Mwachitsanzo, chimanga mudakwenza ndi K300 chonsecho alimi a chimanga amagula fetereza otchipa wa sabuside pomwe alimi a fodya amagula fetereza okwera mtengo kwambiri,” adatero a Zakaliya.

Koma a Chakwera adati mitengo ya fodya amatsitsa okha kaamba kosasamala fodya wawo makamaka posankha ndi podinda m’mabelo chifukwa boma limakhala litasosa kale za mitengo msika usadatsegulidwe.

Potsegulira msikawo, fodya wambiri amagulidwa pakati  pa $1.50 (pafupifupi K1 545) ndi $2.80 (pafupifupi K2 884) kuposa mtengo wa boma wa $1.25 (pafupifupi K1 287) ngati mtengo wapoyambira.

A Chakwera adati boma limayesetsa kukambirana ndi makampani ogulawo za mitengo ya fodya koma mkatikati mwa msika mitengo imayamba kutsika chifukwa ogulawo amaona kuti fodyayo sakuoneka momwe amayembekezera.

“Fodya akamakhala w o s a s a k h a b w i n o , tiziwapatsa powiringulira makampani ogula. Tiyeni tiziyambira kumunda kwathuko kukonza zinthu kuti tikamafika kuno tizikhala ndi mphamvu ponenerera mitengo,” adatero a Chakwera.

Kadaulo pa malonda a fodya a Graham Kunimba adati boma likapanga mtengo woyambira, makampani amayenera kugula pamtengowo kapena kuposa pamenepo.

Koma iwo adati nthawi zambiri pa msika wa okushoni, makampani amakhala akulimbirana fodya ponena mitengo yomwe akuona kuti ikugwirizana ndi mtundu wa fodyayo.

“ N d i y e c h o m w e chimachitika n’choti makampani akasanthula belo n’kuona kuti fodyayo ngosakaniza amapereka mtengo wotsika kapena amangokaniratu belo limenelo,” adatero a Kunimba.

Mkulu woyang’anira msika wa Lilongwe a Samuel Mkutche adati mitengo ya chaka chino ndi yopereka chiyembekezo chabwino kwa alimi poyerekeza ndi mitengo yotsegulira msikawo mmbuyomo.

Iwo adati chaka chino dziko la Malawi likhoza kupeza ndalama zambiri kuchokera m’fodya chifukwa chaka chino kuli fodya wambiri komanso wafika kale wochuluka kumsikawo.

“Panopa fodya yemwe wafika tikhoza kuugulitsa masiku atatu pomwe mmbuyomo sizimachitika ayi. Pali zifukwa ziwiri, choyamba mvula idagwa bwino komanso boma lidachedwetsa dala kutsegula msika kuti ufike wambiri,” adatero a Mkutche.

Chaka chino dziko la Malawi likuyembekeza fodya wokwana makilogalamu 126 miliyoni kuchoka pa fodya wokwana makilogalamu 85 miliyoni chaka chatha.

Chaka chatha msika wa fodya udapeza ndalama zokwana K170 biliyoni kuchokera ku makilogalamu 85 miliyoni a mitundu yonse ya fodya omwe adagulidwa ndipo bungwe loyendetsa za malonda a fodya la Tobacco Commission (TC) lidadandaula chifukwa chakuchepa kwa fodyayo.

Potsegulira msikawo, fodya wabwino kwambiri wa okushoni ankagulidwa pamtengo wa $1.45 (pafupi fupi K1 493) pa kilogalamu pomwe wotsikitsitsa mtengo ankagulidwa pa $0.95 (pafupifupi K978) pa kilogalamu.

Alimi a kontilakiti ndiwo adayamba ndi mitengo yabwino ya $2.30 (pafupifupi K2 369) fodya wabwino kwambiri ndi $0.95 (pafupifupi K978) pa kilogalamu iliyonse ya fodya otsikitsitsa mtengo.

Malingana ndi bungwe la TC, fodya wa 2022 adatsika ndi makilogalamu 31.3 pa makilogalamu 100 alionse poyerekeza ndi fodya okwana makilogalamu 123.7 miliyoni yemwe adagulidwa mu 2021.

The post  Mpungwepungwe ku msika wa fodya first appeared on The Nation Online.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください