Membala wa UTM alipira K5 million kaamba koluma mphuno ya membala wa MCP

Alick Saini, omwe ndi mtsogoleri wa chipani Cha UTM ku Kasungu awagamula kuti apeleke K5 050 000 ngati chindapusa atapezeka olakwa pa mlandu oluma ndi kudula mphuno ya mtsogoleri wa achinyamata a chipani cha MCP, a Chisomo Kefa.

A Saini adapalamula mlanduwu pa 1 September chaka chino atasemphana chichewa ndi a Kefa pa nkhani za pa chiweniweni.

Mwa ndalamazi K4.5 miliyoni ndi chipukuta misonzi chopitsa kwa Kefa pomwe K550,000 ndi yopita ku boma.

Asaini akuyenera kupereka K1.5 miliyoni kwa a Kefa komanso K550,000 ku boma lero kuti awamasule ndipo ndalama yotsalayo awapatsa miyezi isanu kuti amalize.

Magistrate Jones Masula wabwaloli wati wapereka chilangochi chifukwa zomwe adachita a Saini zidapereka chilema chamuyaya kwa a Kefa.

The post Membala wa UTM alipira K5 million kaamba koluma mphuno ya membala wa MCP appeared first on Malawi Voice.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください