MDIMA WATIKUTA: John Tembo wamwalira

Thambo lagwa ndipo m’dima wakuta dziko la Malawi, Mtsogoleri wopuma wa chipani cha Malawi Congress (MCP), a John Zenus Ungapake Tembo (JZU), amwalira.

Mwana wawo, John Tembo Jnr, watsimikiza ponena kuti bambo akewa amwalira m’mawa uno pa chipatala china m’zinda wa Lilongwe komwe anagonekedwa Lolemba sabata yatha.

John omwe anali m’modzi mwa andale opuma m’dziko muno anabadwa pa 14 m’mwezi wa February mu 1932 ndipo amachokera kum’mwera kwa boma la Dedza.

Bambo awo, a Zenus Ungapake Tembo, anali Mtumiki wa mpingo wa CCAP-mu synod ya Nkhoma.

JZU anachita maphunziro ake a primary m’sukulu zosiyanasiyana asanachite maphunziro a sekondale muzinda wa Blantyre pa Blantyre Secondary School (BSS).

kenako, anapita m’dziko la Lesotho komwe adachita maphunziro aukachenjede pa University of Roma(Pius XII College) otchedwa Bachelor’s degree in political philosophy.

Anamaliza maphunziro aukachenjedewa (graduated) m’chaka cha 1958.

Zimamvekanso kuti a Tembo anali ndi maphunziro ena (postgraduate studies) okhudza kayendetsedwe kachuma ndi kuwerengera ndalama omwe anachita ku Britain ndi France.

The post MDIMA WATIKUTA: John Tembo wamwalira appeared first on Malawi Voice.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください