Apolisi kwa Jenda akusunga mchitokosi njonda ina yazaka 33 zakubadwa yomwe inapezeka itabisala kudenga la sitolo ndipo anachita kuthira utsi wokhetsa misonzi kuti itsakamukeko. Malingana ndi mneneri wa apolisi m’bomali a Macfarlen Mseteka, njondayi yomwe dzina lake ndi Alex Tembo inalowa mu sitolomo yotchedwa Chikwendene Distributors Shop. Njondayi ikuba ndalama inapanga phokoso lomwe alonda anamva. […]
The post Mbava inatsakamuka kudenga komwe inabisala apolisi atathira utsi wokhetsa misonzi appeared first on Malawi 24.