Kuyambira lero ndasintha – Joe Gwaladi

M’modzi wa oyimba mdziko muno Joe Gwaladi yemwe ali m’manja mwa apolisi ku Phalombe wati wasiya kuimba nyimbo zachikunja ndipo tsopano ayamba kuimba nyimbo za uzimu.Woyimbayu yemwe akumusunga mchitokosi kamba komuganizira kuti anavulaza mkazi wake pomumenya wati azidziwika ndi dzina loti “Joe Gwaladi Watsopano.”Iye wayankhula izi kudzera pakanema wina yemwe akuzungulira pa masamba a mchezo oyimba ena atapita kukamuzonda kupolisi komwe iye ali.”Satana ndi yemwe amakondwera kuti tidzimwa mowa ndipo tizivulala. Kuyambira lero ndasintha,” watero Gwaladi.Joe Gwaladi yemwe kwawo ndi ku Mlomba m’mboma la Phalombe anamumanga lolemba atamemya mkazi wake modetsa nkhawa.-MBC ONLINE

The post Kuyambira lero ndasintha – Joe Gwaladi appeared first on Malawi Voice.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください