Mc Mooly Makuni Gondwe yemwe amagwira ntchito kundende ya dziko lino ndi mkazi wake Angela Chikho yemwe ndi msilikari anakulira limodzi pa ubwana wawo.
“Takulira limodzi ndipo tinkacheza tili ana achichepere, koma tinasiyana m’chaka cha 2012,” anatero Mc Mooly.
Koma awiriwo anadzakumananso m’chaka cha 2019 kumapemphero ochezera usiku onse pampingo wa CCAP wa Livingstonia ku Kanengo, mumzinda wa Lilongwe komwe patadutsa kanyengo, ubwenzi wawo unayamba.
Patadutsa zaka ziwiri ali pa ubwenzi, awiriwo anadalitsa ukwati wawo pa 3 September pampingo wa Livingstonia Kanengo CCAP, ndipo madyerero anachitikira kuholo ya sukulu ya sekondale ya Kabwabwa ku Area 25, mzinda wa Lilongwe.
Komatu awiriwo sanayende moyera ayi chifukwa ubwenzi wawo unali woyenderana chifukwa Mc Mooly amakhala mumzinda wa Lilongwe pomwe Angela amagwira ntchito yake ku Moyale, mumzinda wa Mzuzu panthawiyo.
Mc Mooly anadandaula kuti kunali kovuta kukumana pafupipafupi pa yomwe anali pa ubwenzi.
Kupatula apo awiriwo anati zokhoma zina zomwe anakumana nazo pa ulendo wawo wabanja zinali zolankhula za anthu omwe amaona ngati angotengana osadalitsa ukwati wawo.
“Chachikulu timayamika Mulungu kuti zinatheka palibe chomwe chinalepheretsa ngati matenda kapena maliro,” iwo anatero.
Mc Mooly amachokera m’mudzi Makuni, m’boma la Rumphi pomwe Angela amachokera m’mudzi mwa Kainga, m’boma la Ntcheu.
The post Kunali ku ‘night of prayer’ appeared first on The Nation Online.