Kabambe wayendera ma membala a DPP m’chipatala

M’modzi mwa akulu akulu ku chipani cha DPP a Dr Dalitso Kabambe lero analunjika ku Chipatala cha Thyolo komwe anakazonda ma membala a chipanichi ochokera mchigawo chaku mwera amene achita ngozi.

Ma membala-wa achita ngozi lero pamene anali pa ulendo opita ku maliro a Gogo Alindine Galleta ku Thyolo.

Ma membala amene akhudzidwa ndi ngoziyi alipo 15 ndipo 7 akulandila thandizo kuchipatala cha m’boma la Thyolo pamene ena okwana 8 analandila thandizo ndipo abwerera ku nyumba kwao ataonedwa ndi madotolo.

“Tikupempha dzanja la Mulungu lamachilitso kuti likhudze nonse kuti mupeze bwino m’sanga” anatero Dr. Kabambe Poyankhulapo, m’modzi mwa ovulalawa wati Mulungu odziwa kudalitsa adalitse a Kabambe kaamba kochita machawi pamene ma membala achipani cha DPP akumana ndi zovuta

The post Kabambe wayendera ma membala a DPP m’chipatala appeared first on Malawi Voice.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください