A Malawi 45 omwe akugwira ntchito mdziko la Israel awamanga.
Zodiak Online yalemba kuti anthu-wa amangidwa kaamba kothawa kumalo komwe anapita kukagwira ntchito ndikupita kutawuni kukagwira ntchito malo ena opanda chilolezo.
Mtsogoleri wa a Malawi okhala ku Israel a Austin Chipeta watsimikiza za kumangidwa kwa a Malawi-wa omwe amangidwa ndi nthambi yowona zolowa ndi zotuluka mdzikolo dzulo.
A Chipeta awuza Zodiak Online kuti a Malawiwa anathawa ku minda kupita kukampani ina yopanga ma bisiketi.
Malingana ndi Zodiak Online, anthuwa akuyembekezeleka kuwatengela ku khothi.
The post Israel yamanga a Malawi okwana 45 appeared first on Malawi Voice.