Galu wakuda wadutsa

Galu wakuda wadutsa

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ati maboma 23 a m’dziko muno alibiletu chakudya kotero apempha akufuna kwabwino kuti athandizepo kuti anthu apulumuke ku njala.

A Chakwera anena izi potsatira lipoti la komiti yofufuza momwe ng’amba ya El Nino yakhudzira Amalawi, makamaka omwe amadalira ulimi okha pa zosowa zawo za tsiku ndi tsiku, kuphatikizapo chakudya.

Mu minda yambiri chimanga sichidachite bwino chaka chino

Iwo ati maanja odalira ulimi oposa 2 miliyoni akhudzidwa ndi ng’ambayo ndipo bungwe la World Food Programme (WFP), nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzidzi ya DoDMA ndi mipingo ina ayamba kale kugawa chimanga ndi ufa.

“Ng’amba yomwe idabwera ndi mphepo ya El Nino yaononga kwambiri moti maanja pafupifupi 2 miliyoni ali pa chiopsezo chachikulu ndipo akufunika thandizo,” atero a Chakwera.

Amalawi omwe acheza ndi Tamvani ati mmera wambiri udafotera m’minda kotero alibe chiyembekezo chilichonse chokolola moti ena mwa Iwo akulingalira zolowera kudimba kunja kukacha.

A Miriam Zuze a ku Mitundu ku Lilongwe ati amakolola matumba osachepela 15 a makilogalamu 50 pa munda wawo koma chaka chino akukayika ngati angawelukeko ndi matumba asanu.

“Chaka chabwino ndimakolola matumba osachepela 15 koma chaka chino ndikuchita kuopa kupita kumunda. M’mera udayamba bwino koma itangobwera ng’amba ija, chiyembekezo chonse kutheratu,” atero a Zuze.

Wapampando wa komiti ya zamalimidwe ku Nyumba ya Malamulo a Sameer Suleman akhala akulangiza boma kuti livomereze kuti m’dziko muno muli njala kuti ena alowelelepo ndi thandizo.

A Suleman adati kunyengezera kuti m’dziko muno muli chimanga pomwe mulibe n’kuseweretsa miyoyo ya anthu.

“Munthu umalandira thandizo ukavomereza kupelewedwa kwako. Koma izizi zomanamizira ngati zinthu zili bwino pomwe zisali bwino n’kusaganizira anthu,” adatero a Suleman.

Koma nduna ya zamalimidwe a Sam Kawale adatsimikizira Amalawi kuti boma lili ndi pulani yolima chimanga cha mthilira kuti lidzasokelele pomwe padzapelewere.

“Bajeti ilipo kale moti tikungoyembekeza kuti aphungu amalize zokambirana kenako tiyambe kulima. M’dziko muno tili ndi madzi ochuluka moti sitiyenera kumadandaula za njala,” adatsindika a Kawale.

Mkulu wa bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) a Jacob Nyirongo alangiza alimi kuti asazapupulume kugulitsa zokolola zawo asadasunge chakudya chokwanira.

“Pakufunika upangiri chifukwa alimi ambiri amakopeka akaona ndalama. Zimenezi n’zomwe alimi ambiri amadzapezeka kuti alibe chakudya chonsecho adakolola ndiye alangizi akuyenera kugwira ntchito,” atero a Nyirongo.

Dziko la Malawi likufunika chimanga choposa matani 600 000 kuti njala yomwe yaopseza kaleyi isadzabweretse chipele.

The post Galu wakuda wadutsa first appeared on The Nation Online.

The post Galu wakuda wadutsa appeared first on The Nation Online.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください