Pomwe Amalawi akulira ndi vuto la kusowa kwa mafuta a galimoto lomwe laimitsa ntchito zambiri makamaka zodalira mafutawo, anthu ena apezapo geni yotentha paululuwo.
Mwachitsanzo, mavenda akugula mafutawo monga petulo akapezeka pa mtengo wa boma wa K1 746 pa lita n’kumagulitsa kwa Amalawi ozingwa pa mtengo wa K5 000 pa lita.
Koma akadaulo ati izi n’zomwe zalimbitsa kwambiri moyo wa anthu m’dziko muno poti kuti ayende akagwire ntchito kapena akapange bizinesi akuyenera kupereka kawiri mtengo womwe ankakwelera basi miyezi iwiri yapitayo mafutawo asadayambe kusowa.
Kwa miyezi iwiri tsopano, Amalawi akugona mmalo mogulitsira mafuta ndi chiyembekezo kuti mwina mafutawo akhoza kubwera kuti aguleko pamtengo woyenera.
Kusowa kwa mafutawo n’komwe kwatsegula mgodi wa mavenda omwe akulolera kugona mmalo ogulitsira mafutawo kuti akafika agule n’kumagulitsa pamtengo wokwera wobera Amalawi.
Koma mkulu wa nthambi yoyang’anira za mphamvu zamagetsi ndi mafuta ya Malawi Energy Regulatory Authority (Mera) a Henry Kachaje ati nthambiyo yaletsa kugula mafuta m’zigubu kapena magaloni chifukwa iyi ndi njira yomwe mavenda akugwiritsa ntchito.
“Timapereka chilolezo munthu akabwera kudzapempha kuti agule mafuta m’zigubu koma taona kuti mwayiwu walowa chibwana, anthu akugula mafutawo kuti azikagulitsanso mobera anzawo,” atero a Kachaje.
Lachiwiri lapitali, apolisi adalanda zigubu, majenereta komanso mathanki a galimoto ndi njinga zamoto zomwe mavenda amagwiritsa ntchito pogula mafuta ngati azingwa n’cholinga chokagulitsanso pamtengo wokwera.
Mneneri wapolisi ku Lilongwe a Hastings Chigalu adatsimikiza kuti apolisi adalanda majenereta abodza 9, mathanki a galimoto ndi njinga zamoto 12 komanso zigubu zoposa 20 pomwe apolisiwo amayendera mmalo ogulitsira mafuta.
“Tipitiriza ntchito imeneyi kuti mchitidwewu uthe chifukwa ukusokoneza zambiri, ukupangitsa kuti mitengo ya basi ikwere moonjeza anthu n’kumalephera kuyenda, zimenezi n’zosokoneza dziko,” atero a Chigalu.
Mkulu wa bungwe la anthu ogula katundu la Consumers Association of Malawi (Cama) a John Kapito ati n’zomvetsa chisoni kuti pomwe dziko la Malawi likufunika kutukula ntchito za mabizinesi kuti chuma chake chikwere, ntchitozo zimunka pansi chifukwa chakusowa kwa mafuta.
“Timadandaula za magetsi koma tidayamba kuzolowera ndipo makampani adayamba kuzolowera kugwiritsa ntchito majenereta tsopano ndi apa mafuta wolizira majeneretawo akusowanso. N’kumati zinthu zikuyenda?” atero a Kapito.
Izi zidachititsa gulu la mabungwe omenyera anthu ufulu la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) kuchenjeza boma Lachiwiri kuti ngati silipangapo kanthu pavutoli, Malawi ayaka moto.
“Talipatsa bomalo masiku 21 kuti vuto la mafuta a galimoto lithe apo ayi timema Amalawi kuti kuyambira pa 7 December kukhale zionetsero zamnanu,” adatero wapampando wa HRDC a Gift Trapence.
Iwo atinso mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera achotse mkulu wa nkhokwe za boma zosungirako mafuta agalimoto (Nocma) a Hellen Buluma komanso aletse maulendo opanda phindu omwe akungoononga ndalama za boma.
Gulu la HRDC lidali patsogolo ponena kuti yemwe ankayendetsa chisankho a Jane Ansah atule pansi udindo chifukwa chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino sichidayende bwino. Pachisankhocho padagwiritsidwa ntchito zofutira zimene bwalo la milandu pa mapeto pa zonse lidagamula kuti sichidayende bwino ndipo pakhale chibwereza.
Koma ngakhale nduna ya zofalitsa nkhani a Gospel Kazako omwenso ndi mneneri wa boma anena kuti a Chakwera apeza kale mayankho a vutolo ndi mavuto ena omwe ali m’dziko muno, atinso vuto la mafutalo sichikonzero cha boma.
“Tonse tikudziwa gwero la kusowa kwa mafuta kuti ndi nkhondo ya Russia ndi Ukraine komanso mavuto azachuma omwe agwera dziko lonse komabe apulezidenti a Chakwera adatambasula kale njira zomwe akonza kuti vutoli ndi mavuto ena athe,” adatero a Kazako.
The post Ena apeza golide pa vuto la mafuta appeared first on The Nation Online.