‘Chiwerewere chakula kwambiri ku Mwanza, Abambo ambiri ikuyenda m’manja’

Mfumu yaikulu Nthache ya m’boma la Mwanza yati m’chitidwe wa chiwerewere pakati pa atsikana oyendayenda, ena mwa anthu oyedetsa galimoto onyamula katundu komanso anthu ochita malonda pakati pa dziko lino ndi maiko ena kudzera ku chipata cha Mwanza wakula kwambiri.

Mfumu Nthache yati kukhalitsa kwa anthu ochita malonda pa chipata cha Mwanza pamene akufuna kuombola katundu wawo ndi zina mwa zifukwa zomwe zikukolezera mchitidwewu.

“Amuna ena amakhala pano akudikilira mapepala akatundu wawo mpaka sabata imodzi ndiye akaona nkazi samapilira koma kuchita naye zadama. Atsikanawa panopa anabwelera nkhani yake yomweyo ndiye amangoti laponda la mphawi,” inatero mfumu Nthache.

Komabe mfumuyi yati ntchito yomanganso chipata cholowa ndi kutuluka mdziko muno cha Mwanza yotchedwa One Stop Border Post pa chigerezi yomwe cholinga chake ndi kufuna kuti anthu ochita malonda komanso onyamula katundu asamazadikire nthawi yaitali kutenga mapepala a katundu wawo ikazatha izathandiza kuchepetsa nchitidwe wachiwerewere-wu.

Pakadalipano MBC yapeza kuti ena mwa oyendetsa galimoto za mtundu wa truck nthawi zina amatha kukhala pamalowa kwa sabata imodzi akudikilira kuti galimoto zawo zilandire mapepala olowera mdziko muno.

Boma ndi ndalama zokwana K3.2 billion likumanga malo otchedwa One Stop Border Post ku Mwanza ndipo mwazina cholinga chake ndikutukula ntchito za malonda pochepetsa nthawi yomwe eni katundu amadikira pa malow- (Wolemba: Chisomo Break,MBC Online Services.)

The post ‘Chiwerewere chakula kwambiri ku Mwanza, Abambo ambiri ikuyenda m’manja’ appeared first on Malawi Voice.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください