Akadaulo osiyanasiyana ati boma likambirane ndi maiko omwe amathandiza dziko lino pa kusemphana kwawo pa nkhani yokhudza mkulu wabungwe lolimbana n’katangale la Anti-Corruption Bureau (ACB) a Martha Chizuma.
Kazembe woimilira dziko la Amerika ku Malawi a David Young, wa dziko la Mangalande a Sophia Willitts – King komanso mgwirizano wa maiko aazungu (European Union – EU) a Rune Skinnebach adawopseza kuti akhoza kulingalira zoimitsa thandizo lawo ku Malawi chifukwa zomwe boma likupanga polimbana ndi a Chizuma zikukaikitsa kuti ndilokonzeka kuthana n’katangale.
Adakhumudwa ndi kuzunda a Chizuma: a Young
Woimilira EU wati thandizo lochokera ku maiko awo limaperekedwa kumaiko omwe akuonetsa chidwi kulimbana n’katangale komanso omwe akugwiritsa ntchito ndalamazo mosabisa kalikonse.
Koma kadaulo pa kayendetsedwe ka zinthu a Boniface Chibwana ati boma lisachite chidodo kukambirana ndi nthumwi za maiko aazunguzo kuti kusemphana kwawo kusafike poimitsa thandizo ku dziko la Malawi chifukwa ovutika ndi Amalawi osati akuluakulu a boma.
Iwo ati padakali pano, Amalawi akuvutika kale ndi momwe chuma chikuyendera komanso potengera momwe ulimi wachaka chino wayendera, kutsogoloku kukuoneka kuti njala ikhoza kuvuta.
“Mukaonesetsa, ntchito zambiri, makamaka zofikira anthu osauka, thandizo lake limachokera kwa azungu. Lingalirani mapulogalamu a zaumoyo omwe amathandiza ndi azungu. Nanga za maphunziro ngakhale chakudya chimene azungu amathandizapo?” atero a Chibwana.
Zina mwa ntchito zomwe thandizo lake lambiri limachokera kwa azungu ndi yamakhwala otalikitsa moyo kwa anthu omwe ali ndi kachilombo koyambitsa matenda a Edzi (HIV), pulogalamu yolimbana ndi chifuwa chachikulu ndi malungo.
Azunguwo amathandizanso mpulogalamu otukula ulimi ngati bizinesi, opititsa patsogolo ntchito za madyedwe abwino, katemera wamatenda osiyanasiyana monga kolera ndi korona zomwe zidavuta pakatipa komanso kumanga sukulu ndi kupereka zipangizo msukuluzo.
Malingana ndi a Chibwana, mapulogalamu ngati awa ali pachiopsezo ngati azunguwo angaimitse thandizo lomwe amapereka ku Malawi kaamba ka nkhaniyi.
Kadaulo pa zachuma a Betchani Tchereni ati ngati boma silisamala pankhaniyi, dziko la Malawi likhoza kuona mavuto aakulu pankhani zachuma chifukwa ganizo lomwe angapange azungu pankhaniyi ndi nsanamira ya momwe chuma chingayendere.
“ Apapa boma liyenera kulingalira mmene chuma chingayendere chithandizo chikasiya kubwera,” iwo atero.
Nduna ya zofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu ati boma lipitiriza kukambirana ndi oimilira maiko aazunguwo, koma ati zokambiranazo sizichititsa kuti boma ligonje pa kagwiridwe ntchito ka nthambi zake.
Iwo ananena izi atakambirana ndi nduna ya zamalamulo a Titus Mvalo komanso yoona za ubale ndi maiko ena a Nancy Tembo.
Nkhaniyi idatumphuka Lachitatu mlangizi wamkulu wa boma pa zamalamulo a Thabo Chakaka Nyirenda atapempha bwalo lamilandu kuti liimitse chiletso chomwe lidapereka ku bungwe la akadaualo a zamalamulo la Malawi Law Society chololeza a Chizuma kubwelera ku ofesi kwawo ngati mkulu wa bungwe la ACB.
Mlembi mu ofesi ya Pulezidenti ndi nduna a Colleen Zamba adaimitsa pantchito a Chizuma pa ngati mkulu wa ACB koma magulu osiyanasiyana adadzudzula nkhaniyo.
Adatero kazembe wa Amereka a Young: “Zomwe zakhala zikuchitika m’miyezi iwiri yapitayi zokhudza mkulu wa ACB zikukaikitsa zoti boma la Malawi likufunadi kuthana n’katangale. Thandizo lathu limabwera kuti litukule miyoyo ya Amalawi koma ngati katangale akupitilira, Amalawi sangatukuke ndiye tikuyang’anira kuti zitha bwanji.”
Naye Kazembe wa Mangalande a Willitts – King adati dziko la Mangalande ndilokhudzidwa ndi zomwe zikuchitikazi pankhondo yolimbana n’katangale.
Ndipo Kazembe wa EU a Skinnebach adati mgwirizanowo ukugwirizana ndi nkhawa zomwe Kazembe wa dziko la Amereka adanena zokhudza kusokoneza a Chizuma kugwira ntchito yawo mwaufulu.
The post Chithandizo chikhalapo? first appeared on The Nation Online.
The post Chithandizo chikhalapo? appeared first on The Nation Online.