Chala M’mwamba! Chala M’mwamba!: Nduna Yakale M’busa Malison Ndau wabweranso ku DPP

Nduna yakale yofalitsa nkhani mu ulamuliro wachipani cha DPP, M’busa Malison Ndau yemwe anapuma pa ndale wabweleranso kuchipanichi patadutsa masiku 28 atabwera mdziko lino kuchokera ku mangalande.

Gavanala wa DPP mchigawo cha kumvuma Sheikh Imran Ntenje yemwe walandira a Ndau lero pamodzi ndi anthu ena awiri wati kubweranso kwawo kulimbikitsa chipanichi pomwe chikukonzekera chisankho cha mchaka cha 2025.

M’mau ake, M’busa Ndau, wati ndiokonzeka kutumikira utsogoleri wa chipanichi ndi cholinga choti chisankho chikubwerachi DPP izapambane ndikukhalanso chipani cholaluma dziko.

A Ndau anakhalako phungu wachipani cha DPP wadera lapakati m’boma la Ntcheu kuchoka mchaka 2014 kufika 2018 asanasiye ndale.

The post Chala M’mwamba! Chala M’mwamba!: Nduna Yakale M’busa Malison Ndau wabweranso ku DPP appeared first on Malawi Voice.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください