Chakwera amuyamikira potumiza Chilima ku Tanzania

Katswiri pa ndale, Czar Kondowe wayamikira mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus Chakwera potumiza wachiwiri wake, Dr Saulos Chilima kukakhala nawo pa mwambo okumbukira umodzi m’dziko la Tanzania.

Poyakhula ndi wayilesi ya Timveni, a Kondowe ati izi zikuonetseratu ubale wabwino omwe ulipo pakati pa a Chakwera ndi a Chilima.

Kondowe watiso anthu akhala akuyankhula zosiyana-siyana zokhudza ubale wa anthu awiri-wa ndipo izi zithandizira kuchotsa maganizo olakwika omwe anthu amakhala nawo okhudza ubale wa atsogoleri-wa.

Komabe, Kondowe wapempha a Chakwera kuti asasiyire pompa koma apitilize kumawatuma a Chilima mu ntchito zosiyana-siyana.

Aka ndi koyamba kuchokera m’chaka cha 2022 kuwona mtsogoleri wa dziko lino akutuma a Chilima kuti akawaimire kunja kwa dziko lino.

The post Chakwera amuyamikira potumiza Chilima ku Tanzania appeared first on Malawi Voice.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください