Bambo wamangidwa kaamba kothira ‘batire’ mbuzi ku Ntchisi

Apolisi ku Ntchisi amanga Vincent Mwale wa zaka 26, anthu atamupezelera akugonana ndi mbuzi.

Mneneri wapolisi ya Ntchisi Salomy Zgambo wati izi zachitika pa 25 mwezi uno m’mudzi mwa Galang’ande cha mma 12 koloko masana.

Malingana ndi a Zgambo, patsikuli mwini chiwetochi anamva kulira kwa mbuziyi modabwitsa kwambiri kuchoka pomwe anamangilira mbuzi yakeyi.

Zgambo wati  izi zinachititsa mwini chiwetochi kuti akaone chomwe chimachitika ndipo anali odabwa kuona a Mwale atakangalika kuchita zakwaipa ndi mbuzi yawo.

Ndipo oganizilidwawa atazindikira kuti awaona akuchita izi, anathawa pamalopo koma anagwidwa ndi achitetezo cha m’mudzi.

Malingana ndi malipoti ochoka kwa anthu okhala m’derali aka sikoyamba kuti oganizilidwawa agone ndi mbuzi ndiye kaamba kotopa ndi Khalidweli akuti anaganiza zokamupereka ku polisi.

Vincent Mwale amachokera m’mudzi mwa Magana, mfumu yaikulu Vuso Jere m’boma la Ntchisi.

The post Bambo wamangidwa kaamba kothira ‘batire’ mbuzi ku Ntchisi appeared first on Malawi Voice.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください