Nyumba ya Malamulo yavomereza bajeti ya ndalama zokwana K5.998 thililiyoni yoti boma ligwiritse ntchito kuyambira pa 1 April 2024 mpaka pa 31 March 2025.Izi zatheka mbali zonse za m’nyumbayo zitasonyeza kukhutira ndi bajetiyo polingalira kuti ndiyofuna kupeputsa mavuto omwe Amalawi akudutsamo.
Aphunguwo adakambirana za bajetiyo kwa tsiku limodzi ndi theka ndipo Amalawi ena ati zomwe apanga aphunguwo n’zokomela dziko lonse.
Aphungu kusangalala pajeti itadutsa
“Zakhala bwino chifukwa nyengo zomwe tikudutsamo ndiyowawa ndipo ikufunika bajeti kuti tiyambepo kupanga zina ndi zina. Aphungu apanga zokomera Amalawi,” atero a Moses Kaira aku Madisi ku Dowa.
Pounika bajetiyo, aphunguwo sadasinthemo kanthu ngakhale akadaulo ati ndalama zomwe zapita ku kampani ya boma ya Admarc nzochepa poyerekeza ndi nkhawa ya njala.
“Bajetiyo ndiyabwino koma pamafunika ndalama zoonjezera ku Admarc chifukwa tikufunika kugula chimanga chambiri malingana ndi nkhawa ya njalayi,” atero a Sameer Suleman wapampando wa komiti y azaulimi ku Nyumba ya Malamulo.
Koma chomwe aphunguwo abwekera ndi kukweza kwa ndalama ya chitukuko ya Constituency Development Fund (CDF) yomwe yachoka pa K100 milliyoni kufika pa K200 miliyoni.
Koma zokambirana za ulendo uno zidali za miliri chifukwa aphungu angapo adatsala pang’ono kumenyana komanso ena adathamangitsidwa mNyumayo.
Phungu wad era la kumadzulo kwa boma la Chikwawa a Susen Dosi ati bajeti yomwe yadutsayo imayenera kutero potengera mavuto omwe dziko la Malawi likudutsamo.
“Ndikalingalira za ng’amba komanso mavuto ena, kudali kofunika kuti bajeti iyiyi idutse kuti tiyambe kukonzekera. Ngati oyimilira Amalawi, tili ndi udindo waukulu kuonetsetsa kuti anthu athu ali pabwino,” adatero a Dosi.
The post Bajeti ya chaka chino yavomerezedwa first appeared on The Nation Online.
The post Bajeti ya chaka chino yavomerezedwa appeared first on The Nation Online.