Atoht Manje wamwalira  

Mmodzi mwa oyimba chamba cha lokolo Atoht Manje wamwalira atadwala kwanthawi yochepa m’boma la Rumphi komwe amakayimba.

Malingana ndi Saint, mmodzi mwa oyimba omwe anali ndi oyimbayu usiku wathawu ku sukulu yaukachenjede ya Livingstonia ku Laws Campus wati Manje anayamba kudandaula kuti akumva kutentha atamaliza kuyimba pasukulupo kenako anakomoka.

Malipoti akusonyeza kuti pomwe amafika naye kuchipatala cha Livingstonia, oyimbayu anali atatisiya kale.

Manje amadziwika kwambiri ndi nyimbo monga Huwa, Zilibwino komanso Che-Patuma mwazina.-MBC

The post Atoht Manje wamwalira   appeared first on Malawi Voice.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください