Asilamu okwiya awotcha dambwe nyau zili momwemu ku Kasungu

Kusanvana kwabuka dzulo pakati pa gulu la anthu cha achipembedzo chisilamu ndi agule wamkulu pa mudzi wa Mchinga dera la mfumu Njombwa mboma la Kasungu zomwe zachititsa kuti asilamu okwiya atenthe dambwe.

Yemwe waona izi zikuchitika, Paul Dickson wati magulu awiriwa anasemphana chichewa, gule wamkulu atagwira mwana wa mtsogoleri wa chipembedzo cha chisilamu kukalowa naye ku dambwe.

Ndipo lachisanu, guleyo anagwiranso bambo a mwanayo omwe amawadzudzula kuti anamenya m’modzi mwa akunjira pomwe amakatenga mwana wawoyo ku dambwe.

Izi zinachititsa a chipembedzo cha chisilamu kuti apite ku dambwe komweko kukatenga mokakamiza mwanayo ndi shehe wa pa mzikiti wa Bua ndipo kenaka anatentha dambwelo.

Mfumu Njombwa ya mderali yati mphala yake inagamula kuti akunjira amasule mwanayo kaamba koti chipembedzo chake sichilola kulowa gule ndipo anati ndiodabwa kunva kuti kusamvanako kwafika potero pamene nkhaniyo inatha.- ZODIAK ONLINE

The post Asilamu okwiya awotcha dambwe nyau zili momwemu ku Kasungu appeared first on Malawi Voice.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください