Anthu akwa Nyambo m’boma la Kasungu aopsyeza ESCOM

By Topson Banda, Kasungu Community Radio

Anthu okhudzidwa kwa Nyambo m’dera la mfumu ya ndodo Wimbe m’boma la Kasungu aopsyeza kuti akachita m’bindikiro ku maofesi a bungwe la ESCOM m’bomali.

Izi zikudza pomwe anthuwa akhala opanda magetsi kuchokera m’chaka cha 2021, kutsatira kuonongeka kwa transformer yomwe imkaperekera magetsi m’deralo.

Wapampando wa anthuwa a Byson Mwale wati apereka ma sabata awiri okha ku maofesi a bungweli kuti akawaikire transformer ina kapena awatsimikizire tsiku lenileni lomwe adzalandirenso magetsi.

“Ngati sipachitika chilichonse m’masabata-wa, tikamanga msasa ku maofesi komweko. Zaka zachulukitsa asakutiganizira ndipo takhala tikugogoda ku ESCOM koma ata! Siziphula kanthu.

Chaka chatha a ESCOM anadzachotsa transformer yoonongekayo nkutilonjeza kuti ayika ina sabata yomweyo koma mpaka lero kuli zii! Ma bizinesi anthu anaima kale-kale pano tusowa mntengo wogwira,” atero a Mwale koma mokwiya.

Koma engineer wamkulu ku bungweli m’bomali a Blessing Mwafulirwa watsimikiza kuti alandira chikalata cha madandaulocho.

Komabe a Mwafulirwa ati deralo liri pa mndandanda wa madera omwe alandire ma transformer posachedwapa.

The post Anthu akwa Nyambo m’boma la Kasungu aopsyeza ESCOM appeared first on Malawi Voice.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください