Anjata wofuna kugulitsa mwana wake

Anjata wofuna kugulitsa mwana wake

A Chimwemwe Zololo atha masiku 6 m’chitokosi cha apolisi ku Zomba powaganizira kuti amafuna kugulitsa mwana wompeza.

A Zololo akuyembekezereka kukaonekera ku bwalo la milandu komwe akukayankha mlandu, malinga ndi mneneri wa polisi ku Zomba a Aaron Chilala.

An artist’s impression of the arrest

Iwo anati nkhaniyi idachitika Loweruka pa 27 Januwale 2024 pamene a Zololo adaika pamsika mwanayo ndi cholinga choti achepetse mavuto a zachuma pakhomo pawo.

Mneneriyu anati amatsatsa mwanayo yemwe ndi wa zaka ziwiri m’mudzi mwa Njala. Kumeneko akuti kudali wamalonda wina amene adadyerera maso pa malondawo.

A Chilala anapitiriza kunena kuti a Zololo ndi wabizinesiyo adagwirizana kuti akakumane m’mudzimo nthawi ya 4 koloko madzulo kuti akamvane za mtengo.

Koma a Zololo samadziwa kuti wamalondayo wawamenya m’mimba kaamba koti adatsina khutu apolisi kuti adzadzionere okha.

“Tidafika pa malopo ndipo timamva awiriwo akukambirana za mtengo. Sitidachedwe komwe kuwambwandira a Zololo,” adatero Chilala.

Iwo adati atafika kupolisi, adaimbira foni akazi awo kuti azamve zomwe amuna awo achita.

Apolisi adagwira pakamwa mkaziyo akunena m’maso muli gwaa kuti nkhaniyo idayamba kukambidwa kunyumba kwawo kuti aphetse mwanayo.

“Koma mkaziyo adatiuza kuti ganizo lofuna kugulitsa mwana lidachokera kwa mwamunayo ndipo mkaziyo adakana kuti zimenezo zisachitike.

“Mkaziyo adati chifukwa chogulitsira mwanayo kudali kuti akonze mavuto a zachuma amene ali m’banja lawo,” adatero a Chilala.

Lachinayi, a Zololo adakaonekera ku bwalo la milandu ku Zomba komwe adaukana mlanduwo. A khoti auimitsa kaye mpaka pa 8 Feburuwale 2024.

Bambowa, omwe ali ndi zaka 25, amachokera m’mudzi mwa Chimbalanga kwa mfumu Chiwalo m’boma la Phalombe.

The post Anjata wofuna kugulitsa mwana wake first appeared on The Nation Online.

The post Anjata wofuna kugulitsa mwana wake appeared first on The Nation Online.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください