Ana ama 2000 sima level anu- Wikise

“Inu anthu azaka izo! Ana ama 2000 sima level anu, mungothapo ndalama chabe. Inuyo ndinu okwatira ndalamazo kadyeni ndi akazi anu kunyumba.”

Umenewo ndiye uthenga waukulu mu nyimbo yatsopano ya Wikise yomwe akuyitcha kuti, Amolo.

Amolo ndichidule cha a Molotoni, bambo wa mvula zakale, obadwa malemu Kamuzu Banda akadalamula.   

Bamboyi wapeza ndalama za ngongole ya NEEF, koma m’malo mochita chitukuko ndi ndalama ya ngongoleyo, akupezeka kuti akuseweletsa ndalamazo malo azinjoyi ndi ana obadwa Facebook itayamba.

Njonda yachimimba chake Amolo-wo, munyimbomo yachitidwa chipongwe kujambulidwa malichocho, ndipo msungwana wachisodzerayo wawakakamiza kuti amulipire 20 million kwacha kuti asawayalutse.

Nanga a Molo akanatani? Mapeto ake apelekadi.

The post Ana ama 2000 sima level anu- Wikise appeared first on Malawi Voice.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください