Amayi ku Chiradzulu akukana kugwiritsa ntchito makondomu

….Ati amaononga chisangalalo ku chipinda pogagadana!

Zadziwika kuti amayi ambiri m’boma la Chiradzulu sakonda kugwiritsa ntchito makondomu achizimayi zomwe zikupangitsa kuti makondomu-wa adziwonongeka.

Izi zadziwika pa mkumano waatsogoleri osiyanasiyana omwe amaunika m’mene akugwilira ntchito pa nkhani zokhudza HIV m’boma la Chiradzulu.

Glory Shaba, yemwe ndi mkulu oyang’anira ndondomeko yogawa makondomu m’bomali, wati pa Chipatala cha m’bomali makondomu amayi akumapanga “expire” asanagwiritsidwe ntchito.

Malingana ndi a Shaba, izi ndi kammba koti amayi ambiri sakumapita ku chipatalachi kuti akatenge makondomuwo.

M’mawu ake Shabam wati vutoli lakula chifukwa choti adindo sakutengapo gawo kwenikweni kufalitsa ubwino ogwilitsa ntchito makondomuwa.

The post Amayi ku Chiradzulu akukana kugwiritsa ntchito makondomu appeared first on Malawi Voice.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください