Khoti la majisitileti m’boma la Dowa lamanga mbusa wina Bonwell Sinoya wa zaka 36 kukagwira ntchito yakalavula gaga kwa zaka 5 pa mlandu wofuna kugwiririra msungwana wa zaka 12 yemwe amamusunga pakhomo pake.
Malingana ndi woimira boma pa milandu a Benedicto Mathambo, mkuluyu adayesa kugwiririra msungwanayo ulendo uwiri azakhali a msungwanayo omwe ndi mkazi wa mbusayo akachokapo.
Iwo adati msungwanayo ataona kuti chiopsezo chikukula, adauza anzake ena zomwe zimamuchitikira kenako anzakewo adamulangiza kuti akauze eni nyumba yomwe banja la mbusayo limachita lendi.
A Mathambo ati a Sinoya adakana mlanduwo mu khoti koma boma lidabweretsa mboni 6 zomwe zidaikira kumbuyo msungwanayo ndipo a Sinoya adapezeka wolakwa pa mlandu wogwira mwana malo olakwika zomwe zimatsutsana ndi gawo 137 ya malamulo.
“Iizi zidayamba kuchitika mwezi wa August 2022 komanso mu March 2023. Akuti mbusayo akazi ake akachokapo, amakalowa kuchipinda komwe msungwanayo amagona n’kumamugwiragwira mosayenera koma masiku onsewo akuti msungwanayo adakana kugonana ndi abusawo,” adatero a Mathambo.
Koma a Mathambo atapempha khoti kuti adagamula kuti a Sinoya akasewenze zaka 5 ku ndende.lipereke chilango chowawa, First Grade Magistrate M’ndala
Womenyera ufulu wa ana a Memory Chisenga adati chilangocho n’chochepa poyerekeza ndi momwe abambo akugwiririra asungwana ndipo adati izi zikukula chifukwa nkhanizi zimathera pa khoti la majisitileti lomwe lili ndi mlingo wochepa popereka zilango.
“Milandu iyiyi imayenera kuti izipita ku khoti lalikulu lomwe lili ndi mphamvu zambiri popereka zilango. Taganizani zaka zisanu zokha kwa munthu yemwe cholinga chake chidali kuononga tsogolo la mwana. Chonchi abambo ena sangakhale ndi mantha,” adatero a Chisenga.
Iwo adapitiriza kuti pomwe zinthu zidafika tsopano, amayi samayenera kukhulupilira bambo aliyense pa chitetezo cha mwana wa mkazi chifukwa ambiri omwe akutchuka ndi nkhani zotere akumakhala abale ake a mwanayo.
Iwo amanena izi polingalira kuti abusawo ankapalamula mlanduwo akazi awo akachoka pakhomo ndipo amasiya msungwana m’manja mwa abusawo osadziwa chomwe chidali mu mtima mwawo.
“Akaka sikoyamba kumva kuti mtumiki wa Mulungu wapanga zoterezi ndipo kunena mosapsatira, ana athu aakazi siali otetezedwa pokhapokha titapeza njira zina zoti mwina tiziwaphunzitsa momwe pawokha angadzitetezere,” adatero a Chisenga.
Iwo adatinso onse ogwira ntchito zoteteza ana akuyenera kuombana mitu ndi kugwirizana momwe chitetezo cha ana makamaka asungwana chingakhwimitsidwire kuti makolo azikhala ndi mtendere m’mitima mwawo ana awo akapita ku sukulu kapena kwina kulikonse.
Chaka chatha, omenyera ufulu wa ana komanso magulu a amayi ndi abambo ena adachita zionetsero zokwiya msungwana wa zaka 14 atagwiriridwa m’chitokolosi cha polisi ndi wapolisi.
Anthu ndi maguluwo adakwiya kuti msungwanayo adagwiriridwa kumalo komwe amayenera kulandira chitetezo komanso ndi munthu woyenera kumuteteza adagamula kuti a Sinoya akasewenze zaka 5 ku ndende.lipereke chilango chowawa, First Grade Magistrate M’ndala
Womenyera ufulu wa ana a Memory Chisenga adati chilangocho n’chochepa poyerekeza ndi momwe abambo akugwiririra asungwana ndipo adati izi zikukula chifukwa nkhanizi zimathera pa khoti la majisitileti lomwe lili ndi mlingo wochepa popereka zilango.
“Milandu iyiyi imayenera kuti izipita ku khoti lalikulu lomwe lili ndi mphamvu zambiri popereka zilango. Taganizani zaka zisanu zokha kwa munthu yemwe cholinga chake chidali kuononga tsogolo la mwana. Chonchi abambo ena sangakhale ndi mantha,” adatero a Chisenga.
Iwo adapitiriza kuti pomwe zinthu zidafika tsopano, amayi samayenera kukhulupilira bambo aliyense pa chitetezo cha mwana wa mkazi chifukwa ambiri omwe akutchuka ndi nkhani zotere akumakhala abale ake a mwanayo.
Iwo amanena izi polingalira kuti abusawo ankapalamula mlanduwo akazi awo akachoka pakhomo ndipo amasiya msungwana m’manja mwa abusawo osadziwa chomwe chidali mu mtima mwawo.
“Akaka sikoyamba kumva kuti mtumiki wa Mulungu wapanga zoterezi ndipo kunena mosapsatira, ana athu aakazi siali otetezedwa pokhapokha titapeza njira zina zoti mwina tiziwaphunzitsa momwe pawokha angadzitetezere,” adatero a Chisenga.
Iwo adatinso onse ogwira ntchito zoteteza ana akuyenera kuombana mitu ndi kugwirizana momwe chitetezo cha ana makamaka asungwana chingakhwimitsidwire kuti makolo azikhala ndi mtendere m’mitima mwawo ana awo akapita ku sukulu kapena kwina kulikonse.
Chaka chatha, omenyera ufulu wa ana komanso magulu a amayi ndi abambo ena adachita zionetsero zokwiya msungwana wa zaka 14 atagwiriridwa m’chitokolosi cha polisi ndi wapolisi.
Anthu ndi maguluwo adakwiya kuti msungwanayo adagwiriridwa kumalo komwe amayenera kulandira chitetezo komanso ndi munthu woyenera kumuteteza
golowa
The post Amanga mbusa wofuna kupumira pa mwana appeared first on The Nation Online.