Alira atamasulidwa

Alira atamasulidwa

Misonzi inagwa kuti lakataaaa! m’masaya a Dennis Dias ngati namondwe bwalo la Senior Resident Magistrate ku Mangochi  litawamasula pa mlandu omwe amayankha powaganizira kuti anagona ndi mwana wa mkazi wa zaka 15.

A Dias omwe ndi a zaka 56 ndi mwini wake wa malo ogona alendo, a Neptune Lodge ku Namwera, T/A Jalasi m’bomalo.

A Dias (Pakati) adakhetsa m’khoti atapatsidwa ufulu

Malingana ndi woimirira milandu wa boma, a Amos Mwaswe, a Dias ankaganiziridwa kuti adathetsa ludzu lawo la chilengedwe pogona ndi mwanayu kumalo awo wochitira malonda a Neptune.

“Iwowa anamukakamiza mwanayu kuti agone naye pong’amba zovala zake zamkati pa 21 May 2023 m’kachipinda kena kumalo awo agona alendowa,” a Mwaswe adafotokoza m’bwalolo.

Koma a Dias ataonekera m’bwalo la mlanduwu, anakanitsitsa kwa mtu wa galu amvekere iwo sanachite izi ndipo pa moyo wawo sanagonepo ndi mwana wachichepere chotero.

Ndipo mwa m’mangummangu pofuna kutsimikizira kusalakwa kwao, a Dias adapeza katswiri pa nkhani yopimapima matupi ndi mitembo, a Charles Dzamalala kuti awathandize kupima thupi la mwanayu pofuna kupeza zoona zenizeni.

Zotsatira za a Dzamalala zidaonetsa kuti a Dias sakukhudzidwa ndi kugona ndi mwanayo, ndipo mmalo mwake zidaonetsa za abambo ena anayi osiyana.

Popereka chigamulo, woweruza mlandu  Muhammad Chande anati bwalo lalephera kupeza umboni weniweni woti mkuluyu ngolakwa kotero anati a Dias ndi mfulu.

Ndipo atangopereka chigamulo, a Dias omwe amachokera m’mudzi mwa Sumaili, m’dera lomwelo m’bomalo anatuluka panja pa khoti akulira uku akuyang’ana kumwamba komanso akufinya kolona kuona ngati bwalolo likunama.

Atatuluka panjapa, analumphalumpha ngati chirombo cha gulewamkulu uku akuzungulira ngati nguli kuli kusangalala.

Wowaimilira mlandu, a Patrick Henry Debwe anati iwo ndi wokondwa kuti chilungamo chachitika ndipo pa tsikulo kukhala chaka kwa Dias kukondwerera ndi chigamulochi.

The post Alira atamasulidwa first appeared on Nation Online.

The post Alira atamasulidwa appeared first on Nation Online.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください