Kampani ya boma yogula ndi kugulitsa mbewu ya Admarc yati iyamba kugula chimanga mwezi wa mawa wa May ndipo yati yakonzeka kugwira ntchitoyo.
Mkulu wa kampaniyo a Rhyno Chiphiko adanena izi Lachitatu unduna wa zamalimidwe utalengeza mitengo yogulira mbewu chaka chino ndipo mbewu ya tsabola wa kapiripiri ndiyo ili ndi mtengo wokwera wa K1 500 pa kilogalamu.
A Chiphiko adati ngakhale boma silidawapatsebe ndalama zogulira mbewu, kampaniyo yapatsidwa chilolezo chobwereka ndalama zokwana K36 biliyoni kumabanki kuti iyambepo kugula mbewu.
“Panopa tili mkati mokambirana ndi mabanki kuti atibwereke ndalama komanso mbali inayi tikukonza mosungira mbewu kuti tikayamba kugula tisasowe kosungira,” adatero a Chiphiko.
Ndipo pulezidenti wa bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) a Frighton Njolomole ayamikira kampaniyo chifukwa chokonzekera msanga kuyamba kugula mbeu kuti iteteze alimi.
“Pamenepa zakhala bwino chifukwa Admarc imapangitsa kuti mavenda asamabele alimi chifukwa Admarc imatsata mtengo wa boma ndiye ngati mavenda akugula mwakuba okha amakwenza mitengo kuti alimbane ndi kampaniyo,” adatero a Njolomole.
Mitengoyo ili motere pa kilogalamu: Chimanga K220, mpunga opuntha K700, mpunga osapuntha K300, mapira K360, mawere 480, soya K480, nyemba zosankha K480, nyemba zoyera K500, nyemba zosasankha K460, mtedza osenda K740, mtedza osasenda K450, khobwe K420,, nandolo K560, mpendadzuwa 450, paprika K900, kapiripiri K1 500, chinangwa K110 ndi thonje K400.
Polengeza mitengoyo, nduna ya zamalimidwe a Lobin Lowe adati popanga mitengoyo, unduna wawo udakambirana ndi Farmers Union of Malawi (FUM), Nasfam, African Institute for Corporate Citizenship (AICC), unduna wa zamalonda, Grain Traders Association of Malawi ndi Indigenous Traders Association.
Mitengo ya mbewu zina chaka chatha idali motere pakilogalamu: Chimanga K150, mpunga openshaw K600, mpunga osapuntha K250, soya K320, mtedza osenda K480, mtedza osasenda K330, nyemba zosankha K510, nyemba zosasankha K410, khobwe K240 ndipo thonje K320.
A Lowe adati makampani akuluakulu komanso abizinesi akunja sakuloledwa kugula nawo mbewu kwa alimi koma iwo adikire mavenda agule kenako agule kwa mavendawo.
Andunawo adapitiriza kuti Amalawi omwe akufuna kugula nawo mbewu akuyenera kutenga chilolezo kuunduna, maofesi a ADD kapena kukhonsolo ya boma lawo ndipo akuyenera kulongosola bwinobwino za komwe azikagulira mbewuzo.
Koma kadaulo pa zamalimidwe a Tamani Nkhono Mvula achenjeza kuti boma lilingalire bwino pa zoletsa makampani akuluakulu kugula mbewu kwa alimi chifukwa likhoza kutsekereza alimiwo kupeza nawo phindu lomwe mavenda apeze pogulitsa ku makampaniwo.
Popanga mitengo yovomerezeka ndi boma, unduna umayang’ana zomwe mlimi adalowetsa kuti akolole kilogalamu imodzi nkuwonjezerapo yapamwamba ngati phindu la mlimiyo.
The post Admarc yakonzeka kugula mbewu appeared first on The Nation Online.