Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ati kuyambira Lachiwiri lapitali adasiya kupereka ntchito kwa wachiwiri wawo a Saulos Chilima ndi cholinga chopereka mwayi woti bungwe lolimbana ndi ziphuphu la Anti-Corruption Bureau (ACB) limasuke pa kafukufuku wawo pa nkhani yokhudza nzika ya ku Mangalande a Zuneth Sattar.
A Chakwera adalengeza izi Lachiwirilo atalandira lipoti la kafukufuku wa ACB pa nkhani ya katangale wa a Sattar ndipo lomwe lidasonyeza kuti anthu 84 adalandira ndalama zankhaninkhani kuchokera kwa iwo mchaka cha 2021.
Samawapatsanso zochita: A Chilima
Malingana ndi lipotilo, a Chilima, mkulu wa polisi m’dziko muno a George Kainja, mkulu woyang’anira nyumba zaboma a Prince Kaponda Mgaga ndi wapampando wa bodi ya nthambi yoona zogula ndi kugulitsa katundu wa boma (PPDA) a John Suzi Banda ndi ena mwa akuluakulu omwe ali pa mndandandawo.
“Polingalira kuti ofesi ya wachiwiri kwa pulezidenti amasankha ndi anthu kudzera mu voti ndipo ine ngati Pulezidenti ndilibe mphamvu zowaimitsa kapena kuwachotsa, ndaganiza zongolanda mphamvu zomwe ndidawapatsa mpaka mapeto a nkhaniyi atadziwika,” anatero a Chakwera.
Malamulo a dziko la Malawi salongosola ntchito za wachiwiri kwa Pulezidenti m’malo mwake, Pulezidenti amachita kuvula zina mwa mphamvu zake n’kupereka kwa wachiwiriyo kuti azimuthandizira ndipo mphamvuzo amatha kuzilandanso nthawi iliyonse.
Izi zikutanthauza kuti a Chilima tsopano azingokhala popanda kugwira ntchito iliyonse ngati wachiwiri kwa Pulezidenti pokhapokha a Chakwera adzabwezeretse mphanvu zomwe awavulazo.
Koma mneneri mu ofesi ya wachiwiri kwa Pulezidenti a Pilirani Phiri ati a Chilima adzalankhula pankhaniyi nthawi yomwe aganize.
Kadaulo pa zamalamulo a Danwood Chirwa ati a Chakwera atsata njira yabwino polanda mphamvuzo kuti anthu komanso dziko lonse lidziwe kuti boma lawo silikusekelera nkhani zakatangale.
“Padali njira ziwiri zoyenera kutsata, yoyamba idali a Chilima eni ake kutula pansi udindo kapena momwe zakhaliramu kuwalanda mphamvu. Iyiyi ndiye njira yabwinoko chifukwa sangathe kuwachotsa pampando ayi,” adatero a Chirwa.
Iwo adamasuliranso kuti ngakhale a Chakwera ali omangika kuchotsa a Chilima pa mpando chifukwa cha nkhaniyi, Nyumba ya Malamulo ili ndi mphamvu zowachotsa litakhutitsidwa ndi zifukwa zake.
Aka nkachiwiri a Chilima kungokhala wachiwiri kwa Pulezidenti koma osamagwira ntchito. Mu mu ulamuliro wa chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) momwenso adali wachiwiri, ankasalidwa pantchito zaboma pazifukwa zomwe sizikudziwika mpaka pano. Iwo adachoka nkuyambitsa chipani chawo cha UTM.
A Chakwera achotsa ntchito a Kainja koma enawa angowaimitsa chabe.
Iwo adadzudzula ndondomeko zogulira katundu waboma zomwe anati zikuchititsa kuti anthu azipeza danga lochita zachinyengo ndi amabizinesi zomwe anati zikufunika kuziunikanso.
Koma a Chakwera ngakhale adati ndiokondwa kuti ACB idapeleka lipotilo mmasiku 21 omwe adalipatsa, sadakondwe ndi lipotilo chifukwa mulibe umboni womwe lidapeza pakafukufuku wake pa anthu omwe adatchulidwa.
“Apapa ndapanga ziganizozi pozindikira kuti Amalawi akufuna kuona tsogolo koma lipoti lomwe ndalandilali silamphamvu ngati momwe limayenera kukhalira. Ndimafuna ACB indipatse umboni woti ndigwiritse ntchito popanga ziganizo ngati zimenezi,” adatero a Chakwera.
Koma iwo adati palibe nduna yawo yomwe idatchulidwa mu lipoti.
The post Achilima awachepetsera mphamvu zaulamuliro appeared first on The Nation Online.