Abusa awaganizira kupereka pathupi

Abusa awaganizira kupereka pathupi

Ali ndi zaka 17, mwanayu ankadwala matenda a muubongo omwe adabweretsanso mavuto olankhula pamoyo wake.

Koma chimodzi chomwe mwanayu amakonda ndi kusonkhana nawo m’malo a mapemphero. Uku ndi komwe mwanayu akuti amapeza chilimbikitso pamoyo wake.

Komatu n’zachisoni kuti kumalo komwe mwanayu amapezako chilimbikitso walandirako mavuto. Wapezeka ndi pathupi pa miyezi inayi ndipo watchula abusa a mpingo wina m’boma la Mzimba kuti ndiwo eni pathupipo.

Msangulutso udafika pakhomo pa mwanayo yemwe amakhala ndi agogo ake ku Mzimbako.

Agogowo adati mwanayo amapemphera kumpingoko ndipo atazindikiridwa kuti ali ndi mimba, adatchula abusawo.

“Nkhaniyo idatikulira ndipo tidakaitula kupolisi komwe adatiyankha kuti popeza mwanayu ali ndi zaka 17, sangatsegule mlandu wogwirira mwana koma tikangosuma kukhoti kuti abusawo azimuthandiza,” anatero abambowo.

Iwo adati adakadula chisamani ndipo nkhaniyi iyamba kulowa m’khoti pa 14 March.

Agogowo adatinso mwanayo amadwala matenda a muubongo kuchokera ali wachichepere omwe amauchititsa kuti nthawi zina azilepheranso kulankhula.

Koma makolowo adati sakukhutitsidwa ndi zomwe adauzidwa kupolisi chifukwa m’dzukulu wawo akadali wamng’ono komanso amadwala matenda a muubongo choncho akufuna abusawo akanazengedwa mlandu ngakhale abusawo anavomera pamaso pa apolisi kuti mimba ndi yawo.

“Ati satana anawanyenga,” adatero abambowo.

Chodabwitsa n’choti abusawo ali ndi udindo waukulu pakati pa abusa a mipingo yonse ku Mzimba ndipo amatenganso gawo lalikulu lophunzitsa zopewa ndi kuteteza ana, achinyamata komanso amayi kunkhanza.

Polankhulapo wogwira ntchito yoteteza ana m’deralo a Washington Phiri anati n’zokhumudwitsa kuti mwanayu wagwiriridwa kachiwiri ndi abambo awiri osiyana.

A Phiri adati n’zodabwitsanso kuti chaka chatha atagwiriridwa makolo a mwanayo adalembetsa kuti ali ndi zaka 15 zomwe zikutanthauza kuti chaka chino amafunika akhale ndi zaka 16.

“Chaka chatha, mwanayu adagwiriridwaponso ndi bambo wina yemwe anathawa nkhaniyi titakaitura ku polisi,” adatero Phiri.

Katswiri pa nkhani zokhudza maufulu a ana komanso amaimira anthu pa milandu yokhudza nkhani za maufulu a Wesley Mwafulirwa adati abusawa akhoza kuzengedwa mlandu wogwiririra munthu wodwala matenda a muubongo.

“Mlandu wochita za dama ndi munthu yemwe pali umboni wokwanira kuti amadwala matenda a muubongo suyendera zaka. Ngakhale zaka zitakhala zambiri, umakhalabe mlandu waukulu malinga ndi malamulo a dziko lino,” adatero a Mwafulirwa.

Nawo akulu apolisi ku Euthini a Rhodes Chitera adati pa nkhani ya zaka za mwanayu makolo ake anenetsa kuti ali ndi zaka 17, zomwe zachititsa kuti apolisi asatsegule mlandu wogwiririra mwana.

“Tidayesetsa kuti tilowerenso kumbali ya matenda a muubongo, koma makolowa anakanitsitsa kuti mwana wawoyo akudwala. Makolowo anangotiuza kuti mwanayo anadwala kwambiri ali wachichepere,” anatero a Chitera.

Apa iwo adatkizanso kuti apolisi akukonza njira zoti mwanayu apite kuchipatala chachikulu mumzinda wa Mzuzu akamuyeze kuti apolisi akhale ndi umboni wogwirika wa matenda ake akamatsegula mlandu.

The post Abusa awaganizira kupereka pathupi appeared first on The Nation Online.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください

コメントを残す

メールアドレスが公開されることはありません。 が付いている欄は必須項目です