Abambo atatu amangidwa kaamba koba mabisiketi

Ku Lilongwe, a polisi amanga anthu atatu powaganizira kuti anakaba mabisiketi ku kampani ya Universal Industries.

Malingana ndi mneneri wa apolisi ya Lilongwe, a Hastings Chigalu, atatu wa akuwaganiziranso kuti anathyola ndikuba katundu wa mnyumba wa ndalama pafupifupi K7.5 million.

Atatu wa ndi Yamikani Sosten wazaka 32 yemwe amadziwikanso kuti “Short”, Martin Lukiya wazaka 38 ndi Dominic Gilbert wazaka 35.

A Chigalu ati apolisi anapita kunyumba kwa mbavazo akuluakulu a kampani ya Universal Industries atakapereka lipoti ku ofesi yawo.

Atafika kunyumbako, apolisiwo anapezanso katundu wina wamnyumba yemwe mbavazo zinaulula kuti zinakaba ku Area 36 ndipo mwini nyumbayo anali asanadziwe kuti kunyumba kwake kwabedwa, ngakhale panali patadutsa tsiku limodzi.

A Chigalu anatsimikiza kuti mwini nyumbayo sanadziwedi kanthu mpaka pomwe apolisiwo anapita kukamudziwitsa kuti waberedwa.

The post Abambo atatu amangidwa kaamba koba mabisiketi appeared first on Malawi Voice.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください