Imodzi mwa makampani ogulitsa zipangizo zomangira m’dziko muno ya Macsteel, yapeleka mphoto ya K1.2 miliyoni kwa bambo wina yemwe wayigwilira ntchito kampaniyi kwa zaka zokwana 40.
Malingana ndi akuluakulu akampaniyi, bambo Biston Mtemankhawa ndiomwe alandira mphatso ya ndalama zokwana K1.2 miliyoni atagwira ntchito ku kampaniyi kuyambira chaka cha 1982.
Akuluakulu a kampaniyi ati bambo Mtemankhawa omwe amagwira ntchito ngati kilinala komaso mesenjala, anali munthu odzipeleka kwambiri pa ntchito yawo komaso amaonetsa makhalidwe abwino.
Macsteel yati yapanga chiganizo chopeleka mphatsoyi pofuna kuthokoza bambo Mtemankhawa komaso ati iyi ndinjira imodzi yolimbikitsira ogwira ntchito ena ku kampaniyi komaso makampani ena zaubwino odzipeleka komaso kukhulupilika panthawi yantchito.
Kampaniyi yatiso ndalamayi siikukhudzana ndi ndalama zomwe munthu amalandira akapuma pa ntchito ndipo yatsindika kuti kupatula ndalamayi, a Mtemankhawa alandiraso ndalama zawo zopumira pa ntchito.
Pakadali pano a Malawi ambiri makamaka pamasamba a mchezo ayamikira kampani ya Macsteel kaamba koonetsa chitsazo chabwino powathokoza a Mtemankhawa ndi ndalamayi
Let us know what you think of this article and remember to add us on our facebook and follow us on our twitter. Come back daily for more Malawi business news.
Quick Links: Download Business eBooks | Ten Signs You Are An Entrepreneur | What is a Managing Director?
The post Macsteel ithokoza ogwira ntchito opuma ndi K1.2 miliyoni – appeared first on Business Malawi.