8 akulimbirana wachiwiri kwa mtsogoleri wa MCP

8 akulimbirana wachiwiri kwa mtsogoleri wa MCP

Ulendo wa ku kovenshoni ya chipani cha Malawi Congress Party (MCP) watentha pomwe mamembala ochuluka asonyeza khumbo lodzapikisana nawo m’mipando yosiyanasiyana.

Ngakhale zili choncho, pampando wa u pulezidenti pali a Lazarus Chakwera okha pomwe anthu 8 akufuna kudzakhala achiwiri kwa a Chakwerawo.

A Mkaka: A Chakwera ali ndi ufulu

Mlembi wamkulu wa chipanicho a Eisenhower Mkaka adatsimikiza kuti ku mkumano wa akuluakulu a chipanicho mu National Executive Committee (NEC) nthumwi zidagwirizana kuti 2025, a Chakwera ndiwo adzaimiire chipani cha MCP pa u Pulezidenti.

“Pokhapo atapezeka wina wofuna kukapikisana nawo a Chakwera ali ndi ufulu koma mgwirizano wathu ukuti a Chakwera ndiwo adzaimire pa u Pulezidenti,” adatero a Mkaka.

Omwe akufuna mpando wa wachiwiri kwa pulezidenti ndi a Catherine Gotani Hara omwe padakalipano ndi mlembi wamkulu wa chipanicho  komanso sipikala wa Nyumba ya Malamulo, a Ahmed Dassu, a Dean Lungu, a Ken Zikhale Ng’oma, a Brown Mpinganjira, a Moses Kunkuyu, a Vitumbiko Mumba ndi a Anderson Moyo.

Mpandowo udakhala opanda mdindo aliyense kuchoka pomwe yemwe adali wachiwiri kwa Pulezidenti m’chipanicho a Sidik Mia adamwalira mmwezi wa January 2021.

Polankhulapo pa zoti NEC idagwirizana kuti a Chakwera ndiwo adzakhale patsogolo, kadaulo pa zandale a George Phiri ati mu demokalase si bwino kukhazikitsa kuti mpando uwu ndi wa uje koma anthu azikhala ndi mpata wopikisana nawo azikalepherera komweko.

“Sizoyenera kukhazikitsa mipando ina ngati yopatulika kwa anthu ena chifukwa mpikisano ndiwo umakonza zofooka osati ena azidziwiratu kuti ali kale ndi mpando ayi,” adatero a Phiri.

Ku kovenshoniyo kudatulukanso mfundo yoletsa alendo kudzaima nawo m’mipando yomwe angafune koma mfundoyo siyidakomere mamembala ambiri ndipo adadzudzula NEC pa ganizolo.

A Phiri ati mfundo yoletsa anthu ena kudzayima nawo mmaudindo nkumana Amalawi mpata wotsogoleredwa ndi anthu omwe akuwawona kuti akhoza kuwathandiza.

“Chomwe chimachitika nchoti anthu akamati akufuna kuima pampando ndiye kuti adaona zofooka ndipo akuona kuti akhoza kukakonza zinthu tsono kuwaletsa kuimako n’kupha tsogolo la dziko,” adatero a Phiri.

Mamembala 102 ndiwo awonetsa khumbo lodzapikisana nawo m’mipando yosiyanasiyana ndipo mmipando yambiri mukupezeka ofuna mpandowo oposa 5.

Ndipo a Phiri ati izi zikusonyeza kuti anthu ayamba kudziwa za ndale za demokalase ndipo adaonjeza kuti mpofunika kuti nthumwi za ku kovenshoni zidzaonetsetse posankha adindowo.

Chichitikileni mkumano wa NEC, anthu akhala akuponya za kampeni ya ofuna kupikisana nawo omwe akuwakhulupirira m’masamba a mchezo ndipo amayi ambiri akuonetsa nawo chidwi chokhala mmipando.

Mmbuyomo, kadaulo wina pa ndale a Ernest Thindwa adati kusankha adindo nthawi ikadali yambiri kumapereka mpata woti chipani chikonzekere bwino chisankho.

Iwo adati kulephera kukonzekera bwino makamaka posankha atsogoleri kukhoza kupangitsa kuti chipani chidzafike nthawi ya chisankho ilibe wochiimirira.

“Komvenshoni ikachitika pamakhala zokola zambiri ndiye pamafunika kuti pakhale nthawi yokwanira yolongosola zokolazo nkumapita bwino chitsoholo,” adatero a Thindwa.

The post 8 akulimbirana wachiwiri kwa mtsogoleri wa MCP first appeared on Nation Online.

The post 8 akulimbirana wachiwiri kwa mtsogoleri wa MCP appeared first on Nation Online.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください