LIKAKUWONA LISILO: Bon Winiko Kalindo wapezeka ndi mfuti

Re-arrested Kalindo

Omenyera ufulu wa anthu m’dziko muno a Bon “Winiko” Kalindo ali ku bwalo la milandu mu mzinda wa Lilongwe komwe akuyankha mlandu omwe anapalamula m’chaka cha 2021 opezeka ndi mfuti opanda chilolezo.

A polisi awuza bwalo la milandu kuti a Kalindo anapezeka ndi mfuti mopanda chilolezo, mu chaka cha 2021.

Padakali pano boma labweletsa m’bwaloli Innocent Kasambara, yemwe ndi wapolisi wakafukufuku.

Kasambara wauza bwaloli kuti akufuna Kalindo akhale mu chitokosi cha apolisi kaamba koti mpaka pano , iwo sanawauzebe apolisi komwe anagula kapena kutenga mfutiwo.

Iye anaonjezera kuti apolisi akufuna Kalindo awalondolere komwe anagula mfutiwo.

Atafunsidwa kuti nchifukwa chani akubweletsa nkhaniyi pano, Kasambara ati kuyambira chaka cha 2021, a Kalindo akhala asakuonetsa chidwi chobweletsa mfutiwo

A Kalindo akuyankha mlandu wu patangotha mphindi zochepa atangotuluka mu bwalo lomweli momwe amafuna apemphe belo pa mulandu wofalitsa uthenga wa bodza.

The post LIKAKUWONA LISILO: Bon Winiko Kalindo wapezeka ndi mfuti appeared first on Malawi Voice.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください