MOTO WA MAPESI: Ken Msonda walowa MCP

M’modzi mwa amene anali mamembala akuluakulu achipani cha DPP, a Ken Msonda, alowa chipani cha Malawi Congress Party (MCP).

A Msonda alandiridwa m’chipani cha MCP ku Mzuzu ndi mtsogoleri wachipanichi, Prezidenti Dr Lazarus Chakwera.

Poyankhula polandira a Msonda, Dr Chakwera adati khomo la chipani cha MCP ndi lotsekula ndipo onse amene akufuna kugwira ntchito ndi chipanichi ndi wolandiridwa.

M’mau awo, a Msonda anati MCP ndi chipani chokhacho chomwe chimatsata mfundo za democracy ndipo ndi okhutira ndi zitukuko zosiyanasiyana zimene zikuchitika m’dziko muno.

A Msonda anapitikisidwa ku chipani cha DPP pamodzi ndi akulu akulu ena monga a Kondwani Nankhumwa kaamba kosowekera mwambo komanso kusalemekeza mtsogoleri wa chipanichi a Peter Mutharika

The post MOTO WA MAPESI: Ken Msonda walowa MCP appeared first on Malawi Voice.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください