A Malawi analozedwa povotera MCP – Mutharika  

Mtsogoleri wakale wa dziko lino a Peter Mutharika ati akukhulupilira kuti a Malawi anachita kupepetulidwa kuti avotere a Lazarus Chakwera pa chisankho cha m’chaka cha 2020.

A Mutharika, omwenso ndi mtsogoleri wa chipani cha DPP, amayakhula izi Lachisanu m’boma la Mangochi.

M’mawu aw, a Mutharika anati kaamba ka kusamva, a Malawi anasankha mtsogoleri yemwe pakadali pano akulephera kuyendetsa bwino chuma cha dziko lino.

Iwo anati adalangiza kangapo konse a Malawi kuti akasankha boma lilipoli ndiye kuti asankha mavuto koma iwo m’malo mwake anatukwanidwa kuti ndi okalamba.

“A Malawi kusamva, kaya kaya munalozedwa kaya ndi chani?…koma ndinakuchenjezani kangapo konse kuti musavotere MCP, koma inu mumandinena ine kuti ndine okalamba komanso opanda mano m’kamwa,” anatero a Mutharika

Malingana ndi a Mutharika chifukwa chosowa masophwenya boma la Chakwera lalephera kupeza ndondomeko zotuluka chuma cha dziko lino.

Pomaliza a Mutharika anati akukhulupilira kuti a Malawi tsopano aphunzirapo ndipo sazachitanso chibwana kuvotera MCP.

The post A Malawi analozedwa povotera MCP – Mutharika   appeared first on Malawi Voice.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください