A Chakwera vumbulukani, a Malawi akufuna mayankho– HRDC

Bungwe lomenyera ufulu wa anthu la HRDC lafunsa mtsogoleli wadziko lino Dr Lazarus Chakwera kuti abwere poyera ndikupeleka mayankho pa vuto la kusowa kwa mafuta m’dziko muno.

Kudzera mu kalata yomwe bungweri latulutsa, ati kukhalachete kwa mtsogoleli wa dziko lino pankhaniyi kukupereka chithunzithunzi chakuti dziko lino lilibe utsogoleri wothekera kubweretsa mayankho pa mavuto omwe nzika zake zikudutsamo.

Wachiwiri kwa wapampando bungweri a Michael Kaiyatsa atiwuza kuti ngati mtsogoleri wadziko lino sabwera poyera ndikupereka mayankho, chuma cha dziko lino chipitirira kulowa pansi ponena kuti malonda omwe amadalira mafutawa akulephera kuyenda..

Posachedwapa, bungwe la MERA linati vutoli lafika pamenepa kaamba kakusowa kwa ndalama zakunja zomwe dziko lino limafuna kuti liyitanitse mafuta kuchoka kunja kwa dziko lino.

The post A Chakwera vumbulukani, a Malawi akufuna mayankho– HRDC appeared first on Malawi Voice.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください