Anthu atatu akhapidwa mpaka kugonekedwa m’chipatala pa mkangano wa ufumu wa nyakwawa Kandanda kwa Senior Chief Kalumo m’boma la Ntchisi.
Potsimikiza nkhaniyo, a Kalumo ati mmodzi mwa okhapidwawo akuyembekezera kukadulidwa dzanja kuchipatala chachikulu cha Kamuzu Central ku Lilongwe.
Naye mneneri wapolisi ku Ntchisi a Yohane Tasowana atsimikiza zankhaniyo ndipo ati nyumba za anthu atatu omwe adakhapidwawo zidagumulidwa ndipo anthu 8 adamangidwa.
“Tamanga anthu 8 ndipo tawatsegulira milandu iwiri, woononga katundu wa eni ndi wina wovulaza anthu. Tikakonzeka tiwatengera kukhoti,” atero a Tasowana.
A Kalumo adati mkanganowo si walero udayamba kalekale kuli ufumu umodzi wokha wa a Kandanda ndipo a Njovu akhala alipansi pa a Kandandawo.
“Ufumu wa a Kandada ndi wakalekale. Nthawi yonseyi a Njovu adali pansi pa a Kandada koma kenako adayamba kuvuta,” atero a Kalumo.
Iwo ati m’zaka za mmbuyomo mkanganowo utakula, iwo adagamula kuti a Njovu akhale ndi wawo ufumu ndipo zidatheka adawaveka ufumuwo m’chaka cha 2018.
“Ndinkaona ngati kupereka ufumu wapadera kwa a Njovu kuthetsa mikanganoyo koma ayi mpomwe zankira patsogolo mpaka kufika pomatemana n’kumagumulirana nyumba,” atero a Kalumo.
Iwo ati mafumu awiriwo ndi ofanana mphamvu koma chomwe bwalo lawo likuona nchoti mtima wa a Njovu umawawa chifukwa salandira mswahara pomwe anzawo a Kandanda amalandira mswahara.
“A Njovu akuvuta kuti ufumu wa a Kandanda utheretu ndipo iwowo ndiwo akhale a mfumu ndiye tikudabwa kuti kodi akufuna ufumuwo kapena nkhani ndi mswahara,” atero a Kalumo.
Iwo ati potsatira mwambo wa ufumuwo, a Kandanda ndiye eni ufumu chifukwa nkwa mayi awo pomwe a Njovu nkwa abambo awo ndipo ufumuwo munthu amakalowa kwa mayi ake.
Mkulu woyang’anira za mafumu ku unduna owona za maboma aang’ono a Charles Makanga ati nkhaniyo ndi yofunika pakhonsolo chifukwa maufumuwo ndi wosankhidwa komweko.
“Unduna umalowelera ufumu wosankhidwa ndi apulezidenti koma wosankhidwa pa khonsolo umathera pakhonsolo pomwepo,” adatero a Makanga.
Uwu ndi mkangano wa ufumu wachiwiri wawukulu chaka chino chokha chifukwa kumayambiliro padalinso mkangano wolimbirana ufumu wa Chikulamayembe m’boma la Rumphi.
Mkangano wa ufumu wa a Chikulamayembe udafika povuta kwambiri mpaka gulu lotsutsana ndi yemwe adavekedwa ufumuwo adagenda galimoto zaboma tsiku lomwe apulezidenti a Lazarus Chakwera adapita kukaveka ufumuwo.
The post Akhapana kaamba ka ufumu ku ntchisi appeared first on The Nation Online.