Wolemba: Gracious Zinazi
Pamene a Malawi akuonetsa kuti anailandira mwa chimwemwe sevisi ya Pamtsetse kuchokera ku TNM komanso MoFaya kuchokera ku Airtel Malawi Plc, zadziwika kuti masevisiwa ndi a miyezi itatu yokha.
Uthenga wa Airtel okhudzana ndi Mofaya
Izi zatsimikizika pomwe kampani ya Airtel Malawi Plc yatulutsa chidziwitso komanso kulemba pa tsamba lake la mchenzo la Twitter pomwe imayankha mmodzi mwa kasitomala wake.
Zomwe Tnm inalemba pa tsamba lake la pa intaneti zikusonyeza kuti Pamtsetse atha mu April
Airtel Malawi Plc inati sevisi ya MoFaya ili pa pulomoshoni yomwe ikuyenera kutha pakatha miyezi itatu kuchokera mwezi watha.
“Chonde dziwani kuti mabandulo a panet MoFaya ali pa pulomoshoni ya masiku makumi asanu ndi anayi (90)” inatero Airtel Malawi Plc mukUyankha kwake.
Pomwe nayo TNM ikuti ma pakeji a Pamtsetse akhazikitsidwa pa pulomoshoni ya miyezi itatu, ndipo ikuyenera kutha pofika mwezi wa April. Kutha kapena kupitirira kwa Pamtsetse sevisi kutengera mmene makasitomala ailandirira sevesiyi.
Anthu ambiri anaonetsa kuti akondwera ndikubwera kwa Pamtsetse komanso MoFaya chifukwa apangitsa mitengo ya mabandulo a itaneti kutsika, pomwe mwachitsanzo ndi K500 Pamtsetse wa TNM anthu akutha kugula bandulo yogwiritsa ntchito pa intaneti kwa tsiku lonse mopanda malire, ndipo panet MoFaya K499 wa Airtel ikumapereka 2GB.
Let us know what you think of this article and remember to add us on our facebook and follow us on our twitter. Come back daily for more Malawi business news.
Quick Links: Download Business eBooks | Ten Signs You Are An Entrepreneur | What is a Managing Director?
The post Pamtsetse ndi MoFaya sanabwere kuzakhala – appeared first on Business Malawi.