An Open Letter to ‘Apule’ Lazarus Chakwera….’Ku ACB kuli Bvumbwe Otantha Patsekera’

Dear Apule,

Some of us never voted for you and olo kamba atadikula will never vote for you for the simple reason that am a Democrat and you are a Republican. It’s a matter of principal and nothing personal.

Unlike that adage which advocates that we must never tell our enemy to do the right thing when they are making a mistake, today I want to take you on to the right path.

Apule, ife pano tili okonzeka kuthana ndi Katangale ndipo nthenda imeneyi tithana nayo koma malingana ndi chibwana chachitika masiku apitawa tikuyenera kuti tikonzenso apo ndi apo.

Apule ntchito sitigwira pa Facebook. Ntchito timagwira mu office, kaya ku field uko ndiko tigwira ntchito. Palibe dziko olo ilo mudapita la Belgium limene limapanga zinthu ati poti facebook yanena.

Kodi izi ndakambiranji? Ine mukuona kwanga ngati munthu amene ndakhala ndikupereka msonkho ochuluka kwambiri kudzera mu PAYE komanso VAT, ine amene ndili ndi chiphaso chanzika yadziko lino, ine amene ndimakhala mdziko lino osati kunja yayi, kwantere nilutsindika ati?

Ndaona kuti kubungwe lothetsa komanso kuthana ndi ziphuphu kwalowa nthenya. Ndati kwalowa zibwana zamchombo lende. Inde apule kuli Bvumbwe otantha patsekera.

Ku Bungwe limeneri APule, kuli anyamata ndi asungwana ogwira bwino ntchito. Iwo ogwira bwino ntchito ayambira monga ija ikhalira nsomba ku mchira mpaka pakhosi. Ayi ikanakhala nsomba ndikanati mchira uli kupukusa bwino mpaka khosi..Koma mutu ndiye wazibwana.

Apule, ife okonda masewero ampira tawonapo akatswiri odziwa bwino lomwe masewera ampira ndipo mwachitsanzo ndikupatseni osewera uyu wankhope yowala Di Maria. Uyu adali osewera wapamwamba ku team ya Madrid.

Iyeyu ankamwetsa zigoli mbambande koma atabwera ku team ya Manchester United mmalo molimbikitsa ukatswiri umene udalipo palibe ndi chimodzi chomwe chimene adachita.

Mungathe kuwona mmene nkhani zakumeneku zikubwelera pa social media kodi pali maturity?

Ine ndikuona ngati mkulu wa corruption alipanoyi basi mumuchotse. Iye adzipita ku Embassy or mumusankhe akakhale Judge mwina angakazigulire ulemu.

Pali anyamata ambiri monga amene angathe kupita kumeneko kukagwira ntchito after all, its team work not individual work. Ngati mukufunanso munthu okhwima panzeru a Judge opuma a Kamanga angathe kukagwira ntchitoyo bwino.

Nthawi ina ndili ku University, tinalinso ndi maloya achizimayi ndipo amphamvu ndithu wina adakhalapo mkulu wa Youth council anthu awa ngati alipo angathe kugwira ntchito yotamandika. They have sufficient level of maturity not zibwana zapa facebook.

Pomaliza Apule mundiperekere moni kwa amathu. Boot anavala ija ndinayikonda moti mwana wanu kuno akuti size 7 ingathe kumukwana.

Katangale ndioyipa ndipo ndi tchimo. Zikufunika munthu okhwima nzeru kuti tithane naye osati munthu wazibwenzi zambirimbiri.

Ndatha Ine,

Pato Phoya

The post An Open Letter to ‘Apule’ Lazarus Chakwera….’Ku ACB kuli Bvumbwe Otantha Patsekera’ appeared first on Malawi Voice.

マラウイニュースメルマガ登録

メルマガ限定配信のマラウイ超ローカルニュースが無料で受け取れます

マラウイ・アフリカ・国際協力に興味があったら登録しよう!

プライバシーポリシーについてはこちらを確認してください

コメントを残す

メールアドレスが公開されることはありません。 が付いている欄は必須項目です